1 Mbiri 23:1-32 NYCCL2016 - Bible AI

1Davide atakalamba, ali ndi zaka zambiri, anayika Solomoni mwana wake kukhala mfumu ya Israeli.

2Iye anasonkhanitsanso pamodzi atsogoleri onse a Israeli, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi.

3Anawerenga Alevi kuyambira a zaka makumi atatu ndi kupitirirapo, ndipo chiwerengero cha amuna onse chinali 38,000.

4Davide anati, “Mwa amenewa, amuna 24,000 aziyangʼanira ntchito za mʼNyumba ya Mulungu ndipo 6,000 akhale akuluakulu ndi oweruza.

5Amuna 4,000 akhale alonda a pa zipata ndipo 4,000 azitamanda Yehova ndi zipangizo zoyimbira zimene ndazipereka ndi cholinga chimenecho.”

6Davide anagawa Aleviwo mʼmagulumagulu motsatira ana a Levi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.

7Ana a Geresoni: Ladani ndi Simei.

8Ana a Ladani:

8Mtsogoleri Yehieli, Zetamu ndi Yoweli. Onse analipo atatu.

9Ana a Simei: Awa anali atsogoleri a mabanja a Ladani.

9Selomoti, Haziyeli ndi Harani. Onse analipo atatu.

10Ndipo ana a Simei anali: Awa anali ana a Semei. Onse analipo anayi.

10Yahati, Zina, Yeusi ndi Beriya.

11Mtsogoleri anali Yahati, ndipo Ziza anali wachiwiri, koma Yeusi ndi Beriya analibe ana aamuna ambiri. Kotero iwo anawerengedwa ngati banja limodzi ndipo anapatsidwa ntchito imodzinso yofanana.

11

12Ana a Kohati:

12Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. Onse analipo anayi.

13Ana a Amramu: Aaroni ndi zidzukulu zake anapatulidwa kwamuyaya kuti azipereka zinthu zopatulika kwambiri monga nsembe pamaso pa Yehova, komanso kuti azitumikira pamaso pake ndi kumadalitsa anthu mʼdzina lake kwamuyaya.

13Aaroni ndi Mose.

14Ana a Mose munthu wa Mulungu anawerengedwa ngati gawo la fuko la Levi.

14

15Ana a Mose:

15Geresomu ndi Eliezara.

16Zidzukulu za Geresomu:

16Mtsogoleri anali Subaeli.

17Zidzukulu za Eliezara: Eliezara analibe ana ena aamuna, koma ana a Rehabiya anali ochuluka kwambiri.

17Mtsogoleri anali Rehabiya.

18Ana a Izihari:

18Mtsogoleri anali Selomiti.

19Ana a Hebroni:

19Mtsogoleri anali Yeriya, wachiwiri anali Amariya, Yahazieli anali wachitatu ndipo Yekameamu anali wachinayi.

20Ana a Uzieli:

20Mtsogoleri anali Mika ndipo wachiwiri anali Isiya.

21Ana a Merari: Ana a Mahili: Eliezara ndi Kisi.

21Mahili ndi Musi.

22Eliezara anamwalira wopanda ana aamuna. Iye anali ndi ana aakazi okhaokha. Abale awo, ana a Kisi, ndiwo amene anawakwatira.

22

23Ana a Musi:

23Mahili, Ederi ndi Yeremoti. Onse analipo atatu.

24Izi zinali zidzukulu za Levi mwa mabanja awo, atsogoleri a mabanja monga momwe analembedwera mayina awo ndi monga momwenso anawerengedwera, banja lililonse pa lokha. Awa ndi anthu ogwira ntchito oyambira zaka makumi awiri zobadwa kapena kupitirirapo, amene amatumikira mʼNyumba ya Yehova.

25Popeza Davide anati, “Pakuti Yehova Mulungu wa Israeli, wapereka mpumulo kwa anthu ake ndipo wabwera kudzakhala mu Yerusalemu kwamuyaya,

26sikofunikiranso kuti Alevi azinyamula tenti kapena zipangizo za chipembedzo.”

27Potsata malangizo otsiriza a Davide, Alevi anawerengedwa kuyambira amuna a zaka makumi awiri zakubadwa kapena kupitirirapo.

28Ntchito ya Alevi inali kuthandiza zidzukulu za Aaroni pa ntchito yotumikira mʼNyumba ya Yehova monga kuyangʼanira mabwalo, zipinda zamʼmbali, kuyeretsa zinthu zonse zachipembedzo, ndiponso kuchita ntchito zina za mʼnyumba ya Mulungu.

29Iwo amayangʼanira buledi amene amayikidwa pa tebulo, ufa wa nsembe yachakudya, timitanda ta buledi wopanda yisiti: kuphika ndi kusakaniza, ndiponso miyeso yonse ndi kukula kwake.

30Iwo amayimiriranso mmawa uliwonse kuthokoza ndi kutamanda Yehova. Amachitanso chomwecho madzulo,

31ndiponso popereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa Sabata ndi pa chikondwerero cha Mwezi Watsopano, ndi pa nthawi yosankhidwa ya Chikondwerero. Iwo amatumikira pamaso pa Yehova nthawi zonse mwa chiwerengero chawo ndi momwe analangizidwira.

32Ndipo kotero Alevi anachita ntchito yawo ya ku tenti ya msonkhano ya ku Malo Opatulika ndiponso molamulidwa ndi abale awo, zidzukulu za Aaroni, pa ntchito ya mʼNyumba ya Yehova.

>