1 Mbiri 6:1-81 NYCCL2016 - Bible AI

1Ana a Levi anali awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.

2Ana a Kohati anali awa:

2Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli.

3Ana a Amramu anali awa: Ana a Aaroni anali awa: Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara

3Aaroni, Mose ndi Miriamu.

4Eliezara anabereka Finehasi,

4Finehasi anabereka Abisuwa,

5Abisuwa anabereka Buki,

5Buki anabereka Uzi.

6Uzi anabereka Zerahiya,

6Zerahiya anabereka Merayoti,

7Merayoti anabereka Amariya,

7Amariya anabereka Ahitubi.

8Ahitubi anabereka Zadoki,

8Zadoki anabereka Ahimaazi.

9Ahimaazi anabereka Azariya,

9Azariya anabereka Yohanani,

10Yohanani anabereka Azariya (uyu ndi amene anatumikira monga wansembe mʼNyumba ya Mulungu imene Solomoni anamanga mu Yerusalemu),

10

11Azariya anabereka Amariya,

11Amariya anabereka Ahitubi,

12Ahitubi anabereka Zadoki,

12Zadoki anabereka Salumu,

13Salumu anabereka Hilikiya,

13Hilikiya anabereka Azariya,

14Azariya anabereka Seraya,

14ndipo Seraya anabereka Yehozadaki.

15Yehozadaki anagwidwa ukapolo pamene Yehova analola Nebukadinezara kuti agwire ukapolo Yuda ndi Yerusalemu.

15

16Ana a Levi anali awa:

16Geresomu, Kohati ndi Merari.

17Mayina a ana a Geresomu ndi awa:

17Libini ndi Simei.

18Ana a Kohati anali awa:

18Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli.

19Ana a Merari anali awa: Mayina a mabanja a fuko la Levi olembedwa potsata makolo awo ndi awa:

19Mahili ndi Musi.

20Ana a Geresomu ndi awa: Zima,

20Libini, Yehati,

21Yowa, ndi Yeaterai.

21Ido, Zera

22Zidzukulu za Kohati ndi izi: Asiri,

22Aminadabu, Kora,

23Elikana,

23Ebiyasafu, Asiri,

24Tahati, Urieli,

24Uziya ndi Sauli.

25Zidzukulu za Elikana ndi izi:

25Amasai, Ahimoti,

26Elikana, Zofai,

26Nahati,

27Eliabu, ndi Samueli.

27Yerohamu, Elikana

28Ana a Samueli ndi awa: wachiwiri anali Abiya.

28Mwana wake woyamba anali Yoweli,

29Zidzukulu za Merari ndi izi: Simei, Uza,

29Mahili, Libini,

30Simea, Hagiya

30ndi Asaya.

31Awa ndi anthu amene Davide anawayika kuti aziyangʼanira mayimbidwe mʼNyumba ya Yehova, Bokosi la Chipangano litabwera kudzakhala mʼmenemo.

32Iwo ankatumikira akuyimba nyimbo pa khomo la malo opatulika, tenti ya msonkhano, mpaka Solomoni atamanga Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu. Iwo ankagwira ntchito zawo potsata malamulo amene anawapatsa.

33Mayina a anthuwo, pamodzi ndi ana awo, anali awa: Ochokera ku banja la Kohati: Hemani, katswiri woyimba, anali mwana wa Yoweli, mwana wa Samueli,

34mwana wa Elikana, mwana wa Yerohamu,

34mwana wa Elieli, mwana wa Towa,

35mwana wa Zufi, mwana wa Elikana,

35mwana wa Mahati, mwana wa Amasai,

36mwana wa Elikana, mwana wa Yoweli,

36mwana wa Azariya, mwana wa Zefaniya,

37mwana wa Tahati, mwana wa Asiri,

37mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora,

38mwana wa Izihari, mwana wa Kohati,

38mwana wa Levi, mwana wa Israeli;

39ndi Asafu mʼbale wake, amene ankatumikira ku dzanja lake lamanja:

39Asafu anali mwana wa Berekiya, mwana wa Simea,

40mwana wa Mikayeli, mwana wa Baaseya,

40mwana wa Malikiya,

41mwana wa Etini,

41mwana wa Zera, mwana wa Adaya,

42mwana wa Etani, mwana wa Zima,

42mwana Simei,

43mwana wa Yahati,

43mwana wa Geresomu, mwana wa Levi;

44ndipo abale awo ena anali a banja la Merari amene amatumikira ku dzanja lake lamanzere: mwana wa Maluki,

44Etani anali mwana wa Kisi, mwana wa Abidi,

45mwana wa Hasabiya,

45mwana wa Amaziya, mwana wa Hilikiya,

46mwana wa Amizi, mwana wa Bani,

46mwana wa Semeri,

47mwana wa Mahili, mwana wa Levi.

47mwana wa Musi, mwana wa Merari,

48Abale awo Alevi anapatsidwa ntchito zina zonse ku malo opatulika ku nyumba ya Mulungu.

49Koma Aaroni ndi zidzukulu zake anali amene amapereka nsembe pa guwa lansembe zopsereza ndi pa guwa lansembe zofukiza pamodzi ndi zonse zimene zimachitika ku malo opatulika kwambiri, kuchita mwambo wopepesera Israeli, potsata zonse zimene Mose mtumiki wa Mulungu anawalamulira.

50Ana a Aaroni ndi zidzukulu zake anali awa: Eliezara, Finehasi, Abisuwa,

51Buki,

51Uzi, Zerahiya,

52Merayoti, Amariya,

52Ahitubi,

53Zadoki

53ndi Ahimaazi.

54Malo amene iwo anapatsidwa kuti likhale dziko lawo ndi awa: (Malowa anapatsidwa kwa zidzukulu za Aaroni zimene zinali za banja la Kohati, chifukwa malo oyamba kugawidwa anali awo).

55Iwo anapatsidwa Hebroni mʼdziko la Yuda ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa.

56Koma minda ndi midzi yozungulira mzindawo zinapatsidwa kwa Kalebe mwana wa Yefune.

57Kotero zidzukulu za Aaroni zinapatsidwa Hebroni (mzinda wopulumukirako), ndi Libina, Yatiri, Esitemowa,

58Hileni, Debri,

59Asani, Yuta ndi Beti-Semesi pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa.

60Ndipo ku fuko la Benjamini anapatsidwa Gibiyoni, Geba, Alemeti ndi Anatoti, pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa.

60Mizinda imene anapatsidwa ku banja la Kohati onse pamodzi inalipo 13.

61Zidzukulu zotsala za Kohati anazigawira midzi khumi kuchokera ku mabanja a fuko la theka la Manase.

62Zidzukulu za Geresomu banja ndi banja zinapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mafuko a Isakara, Aseri ndi Nafutali, ndi gawo lina la fuko la Manase limene lili ku Basani.

63Zidzukulu za Merari banja ndi banja zinapatsidwa mizinda khumi ndi iwiri kuchokera ku mafuko a Rubeni, Gadi ndi Zebuloni.

64Kotero Aisraeli anapatsa Alevi mizindayi ndi madera a msipu ozungulira malowa.

65Kuchokera ku mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini anawapatsa mizinda imene inawatchula kale mayina.

66Mabanja ena a Kohati anapatsidwanso malo kuchokera ku fuko la Efereimu.

67Kuchokera ku dziko lamapiri la Efereimu anapatsidwa Sekemu (mzinda wopulumukirako) ndi Gezeri,

68Yokineamu, Beti-Horoni,

69Ayaloni ndi Gati-Rimoni, pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira.

70Ndipo kuchokera ku theka la fuko la Manase, Aisraeli anapereka Aneri ndi Bileamu pamodzi ndi madera odyetsera ziweto kwa mabanja ena onse a Kohati.

71Ageresomu analandira malo awa: Kuchokera ku theka la fuko la Manase, analandira Golani ku Basani ndiponso Asiteroti, ndi malo awo odyetsera ziweto;

72Kuchokera ku fuko la Isakara

72analandira Kedesi, Daberati,

73Ramoti ndi Anemu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;

73

74kuchokera ku fuko la Aseri

74analandira Masala, Abidoni,

75Hukoki ndi Rehobu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;

75

76ndipo kuchokera ku fuko la Nafutali

76analandira Kedesi ku Galileya, Hamoni ndi Kiriyataimu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto.

77Amerari (Alevi ena onse) analandira madera awa: iwo analandira Yokineamu, Karita, Rimono ndi Tabori, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;

77kuchokera ku fuko la Zebuloni,

78Kuchokera ku fuko la Rubeni kutsidya kwa Yorodani, kummawa kwa Yeriko,

78analandira Bezeri ku chipululu, Yaza,

79Kedemoti ndi Mefaati, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;

79

80ndipo kuchokera ku fuko la Gadi

80analandira Ramoti ku Giliyadi, Mahanaimu,

81Hesiboni ndi Yazeri, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto.