1Davide anayimbira Yehova nyimbo iyi pamene Yehovayo anamupulumutsa mʼdzanja la adani ake onse ndiponso mʼdzanja la Sauli.
2Iye anati,
2“Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga.
3Mulungu wanga ndiye thanthwe langa, mʼmene ndimathawiramo,chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa.Iye ndi linga langa, pothawirapo panga ndi mpulumutsi wanga.Munandipulumutsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.
3
4“Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando,ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga.
4
5“Mafunde a imfa anandizinga;mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri.
6Anandimanga ndi zingwe za ku manda;misampha ya imfa inalimbana nane.
6
7“Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova;ndinapemphera kwa Mulungu wanga.Iye ali mʼnyumba yake, anamva mawu anga;kulira kwanga kunafika mʼmakutu ake.
7
8“Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi,maziko a miyamba anagwedezeka;ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya.
42Iwo anafuwula kupempha thandizo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe owapulumutsa.Analirira kwa Yehova, koma sanawayankhe.
43Ine ndinawaperesa ngati fumbi la pa dziko lapansi;ndinawasinja ndipo ndinawapondaponda ngati matope a mʼmisewu.
43
44“Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa mitundu ya anthu;Inu mwandisunga kuti ndikhale mtsogoleri wa anthu a mitundu ina.Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga.
45Alendo amadzipereka okha pamaso panga;akangomva za ine, amandigonjera.