1Mawu a Amosi, mmodzi mwa anthu oweta nkhosa ku Tekowa. Zimene iye anaona mʼmasomphenya zokhudza Israeli patatsala zaka ziwiri kuti chivomerezi chichitike, nthawi imene Uziya anali mfumu ya Yuda ndipo Yeroboamu mwana wa Yowasi anali mfumu ya Israeli.
2Amosi anati: “Yehova akubangula mu Ziyonindipo akumveka ngati bingu mu Yerusalemu;msipu wa abusa ukulira,ndipo pamwamba pa Karimeli pakuwuma.”
3Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Damasiko akunka nachimwirachimwira,Ine sindileka kuwalanga.Popeza anapuntha Giliyadindi zopunthira za mano achitsulo,
4Ine ndidzatumiza moto pa nyumba ya Hazaeliumene udzanyeketsa nyumba zaufumu za Beni-Hadadi.
5Ndidzathyola chipata cha Damasiko;ndidzawononga mfumu yokhala ku Chigwa cha Aveni,ndiponso iye amene akugwira ndodo yaufumu mu Beti-Edeni.Anthu a ku Aramu adzapita ku ukapolo ku Kiri,”akutero Yehova.
6Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Gaza akunka nachimwirachimwira,Ine sindileka kuwalanga.Popeza anatenga ukapolo mtundu wathunthundi kuwugulitsa ku Edomu,
7ndidzatumiza moto pa makoma a Gazaumene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu.
8Ndidzawononga mfumu ya ku Asidodikomanso amene akugwira ndodo yaufumu ku Asikeloni.Ndidzalanga Ekroni,mpaka wotsala mwa Afilisti atafa,”akutero Ambuye Yehova.
9Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Turo akunka nachimwirachimwira,Ine sindileka kuwalanga.Popeza iwo anagulitsa mtundu wathunthu ku ukapolo ku Edomu,osasunga pangano laubale lija,
10Ine ndidzatumiza moto pa makoma a Turoumene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu.”
11Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Edomu akunka nachimwirachimwira,Ine sindileka kuwalanga.Popeza anathamangitsa mʼbale wake ndi lupanga,popanda nʼchifundo chomwe.Popeza mkwiyo wake unakulabendipo ukali wake sunatonthozeke,
12Ine ndidzatumiza moto pa Temaniumene udzanyeketsa nyumba zaufumu za Bozira.”
13Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Amoni akunka nachimwirachimwira,Ine sindileka kuwalanga.Popeza anatumbula akazi oyembekezera a ku Giliyadinʼcholinga choti akuze malire awo,
14Ine ndidzayatsa moto pa makoma a ku Rabaumene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu.Padzakhala kulira kwakukulu pa tsiku la nkhondoyo,kumenyana kudzakhala kwafumbi ngati mkuntho wa kamvuluvulu.
15Mfumu yawo idzatengedwa kupita ku ukapolo,iyo pamodzi ndi akuluakulu ake,”akutero Yehova.