9Lengezani zimenezi ku nyumba zaufumu za ku Asidodindiponso ku nyumba zaufumu za ku Igupto:“Sonkhanani ku mapiri a ku Samariya;onani chisokonezo pakati pakendiponso kuponderezana pakati pa anthu ake.”
9
10“Iwo sadziwa kuchita zolungama,ndipo amadzaza malo awo otetezedwa ndi zinthu zolanda ku nkhondo ndi zakuba,” akutero Yehova.
11Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akunena izi: “Mdani adzalizungulira dzikoli;iye adzagwetsa malinga ako,ndi kufunkha nyumba zako zaufumu.”
12Yehova akuti, “Monga mʼbusa amalanditsa mʼkamwa mwa mkangomiyendo iwiri yokha kapena msonga yokha ya khutu,moteronso ndimo mmene adzapulumukire Aisraeliamene amakhala mu Samariyapa msonga za mabedi awo,ndi ku Damasiko pa akakhutagona awo.”
13“Imvani izi ndipo mupereke umboni wotsutsa nyumba ya Yakobo,” akutero Ambuye, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse.
14“Pa tsiku limene ndidzalange Israeli chifukwa cha machimo ake,ndidzagumula maguwa ansembe a ku Beteli;nyanga za guwa zidzathyokandipo zidzagwa pansi.
15Ndidzagwetsa nyumba ya pa nthawi yozizirapamodzi ndi nyumba ya pa nthawi yotentha;nyumba zokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu zidzawonongedwandipo nyumba zikuluzikulu zidzaphwasulidwa,”akutero Yehova.