10Maphwando anu achipembedzo ndidzawasandutsa kulira kwa chisonindipo kuyimba kwanu konse ndidzakusandutsa maliro.Ndidzakuvekani chiguduli nonsenundi kumeta mipala mitu yanu.Nthawi imeneyo idzakhala ngati yolira mwana wamwamuna mmodzi yekhayo,ndipo tsikulo lidzakhala lowawa mpaka kutha kwake.
10
11“Nthawi ikubwera,” Ambuye Yehova akunena kuti,“Ndidzagwetsa njala mʼdziko lonse;osati njala ya chakudya kapena ludzu la madzi,koma njala yofuna kumva mawu a Yehova.
12Anthu azidzangoyendayenda kuchoka ku nyanja ina kupita ku nyanja ina.Azidzangoyendayenda kuchoka kumpoto kupita kummawa,kufunafuna mawu a Yehova,koma sadzawapeza.
13“Tsiku limenelo “anamwali okongola ndi anyamata amphamvuadzakomoka ndi ludzu.
14Onse amene amalumbira pa tchimo la Samariya,kapena kumanena kuti, ‘Iwe Dani, pali mulungu wako wamoyo,’kapena, ‘Pali mulungu wamoyo wa ku Beeriseba.’Iwowo adzagwandipo sadzadzukanso.”