1Ine ndinaona Ambuye atayima pambali pa guwa lansembe, ndipo anati: “Kantha mitu ya nsanamirakuti ziwundo za nyumba zigwedezeke.Muzigwetsere pa mitu ya anthu onse,onse amene atsalira ndidzawapha ndi lupanga.Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathawe,palibe amene adzapulumuke.
2Ngakhale atakumba pansi mpaka ku malo a anthu akufa,dzanja langa lidzawatulutsa kumeneko.Ngakhale atakwera kumwambaIne ndidzawatsakamutsa kumeneko.
3Ngakhale atakabisala pamwamba pa phiri la Karimeli,Ine ndidzawasaka kumeneko ndi kuwagwira.Ngakhale atakabisala pansi pa nyanja yayikulu,ndidzalamula njoka kuti iwalume kumeneko.
5Ambuye Yehova Wamphamvuzonseamene amakhudza dziko lapansi ndipo dzikolo limasungunuka,onse amene amakhala mʼmenemo amalira.Dziko lonse lidzadzaza ngati mtsinje wa Nailo,kenaka nʼkuphwera ngati mtsinje wa ku Igupto.
6Iye amene amamanga malo ake okhalamo kumwamba,ndi kuyika maziko ake pa dziko lapansi,Iye amene amayitana madzi a ku nyanjandikuwakhuthulira pa dziko lapansi,dzina lake ndiye Yehova.
6
7“Kodi kwa Ine, inu Aisraeli, simulichimodzimodzi ndi Akusi?”Akutero Yehova.“Kodi sindine amene ndinatulutsa Israeli ku Igupto,Afilisti ku Kafitorindi Aaramu ku Kiri?
7
8“Taonani, maso a Ambuye Yehovaali pa ufumu wochimwawu.Ndidzawufafanizapa dziko lapansi.Komabe sindidzawononga kotheratunyumba ya Yakobo,”akutero Yehova.
9“Pakuti ndidzalamula,ndipo ndidzagwedeza nyumba ya Israelipakati pa mitundu yonse ya anthumonga momwe amasefera ufa mʼsefa,koma palibe nʼkamwala kamodzi komwe kamene kadzagwe pansi.
10Anthu onse ochimwa pakati pa anthu angaadzaphedwa ndi lupanga,onse amene amanena kuti,‘Tsoka silidzatigwera ife kapena kutiwononga.’
11“Tsiku limenelo ndidzabwezeretsanyumba ya Davide imene inagwa.Ndidzakonzanso malo amene anagumuka,ndi kuyimangansomonga inalili poyamba,
12kuti adzatengenso otsala a Edomundi mitundu yonse imene imatchedwa ndi dzina langa,”akutero Yehova amene adzachita zinthu izi.