1Vumbulutso lochokera kwa Yesu Khristu, limene Mulungu anamupatsa kuti aonetse atumiki ake zimene zinayenera kuchitika posachedwa. Iye anatuma mngelo wake kuti adziwitse mtumiki wake Yohane,
2amene akuchitira umboni chilichonse chimene anachiona. Awa ndi Mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu Khristu.
3Ngodala munthu amene awerenga mawu oneneratu zamʼtsogolo ndi iwo amene amamva ndi kusunga zolembedwa mʼbukuli pakuti nthawi yayandikira.
4Ndine Yohane,
5ndiponso kuchokera kwa Yesu Khristu mboni yokhulupirika, woyamba kuukitsidwa, ndi wolamulira mafumu a dziko lapansi.
6ndipo watisandutsa mafumu ndi ansembe kuti tizitumikira Mulungu ndi Atate ake. Kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu ku nthawi zosatha, Ameni.
7
8“Ine ndine Alefa ndi Omega,” akutero Ambuye Mulungu Wamphamvuzonseyo “amene muli, amene munalipo, ndi amene mudzakhalapo.”
9Ine Yohane mʼbale wanu ndi mnzanu mʼmasautso ndi mu ufumu ndi mukupirira kwambiri, zomwe ndi zathu mwa Yesu, ndinali pa chilumba cha Patimo chifukwa cha Mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu.
10Pa tsiku la Ambuye ndinanyamulidwa ndi Mzimu ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mawu ofuwula ngati lipenga,
11amene anati,
12Nditatembenuka kuti ndione amene amandiyankhulayo, ndinaona zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zagolide.
13Pakati pa zoyikapo nyalezo ndinaona wina wooneka ngati Mwana wa Munthu atavala mkanjo wofika kumapazi ake ndipo anamangirira lamba wagolide pa chifuwa pake.
14Tsitsi lake linali loyera ngati thonje, kuyera ngati matalala, ndipo maso ake amawala ngati malawi amoto.
15Mapazi ake anali ngati chitsulo choti chili mʼngʼanjo yamoto, ndipo mawu ake anali ngati mkokomo wamadzi othamanga.
16Mʼdzanja lake lamanja ananyamula nyenyezi zisanu ndi ziwiri, ndipo mʼkamwa mwake munali lupanga lakuthwa konsekonse. Nkhope yake imawala ngati dzuwa lowala kwambiri.
17Nditamuona ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa. Kenaka Iye anasanjika dzanja lake lamanja pa ine nati,
18
19
20