3Pakuti mayiko onse amwavinyo ozunguza mutu wazigololo zake.Mafumu a dziko lapansi achita naye chigololo,ndipo amalonda a dziko lapansi analemera kuchokera pa zolakalaka zake zosefukira.”
4Ndiponso ndinamva mawu ena kuchokera kumwamba akuti: “ ‘Anthu anga tulukani, mwa iye,’mungachimwe nayekuti musadzalandire nawo gawo lililonse la miliri yake;
5pakuti machimo ake awunjikana mpaka kumwamba,ndipo Mulungu wakumbukira milandu yake.
6Bwezerani Iye monga momwe iye anakuchitirani.Mubwezereni mowirikiza pa zimene anachita.Mumusakanizire magawo awiri kuchokera mʼchikho chake.
7Mumuzunze, kumumvetsa chisoni kwambirimonga mwaulemerero ndi zolakalakazimene anadzaza mu mtima mwake. Iye anadzikuza nʼkumati,‘Ndinakhala monga mfumu yayikazi,ine sindine wamasiyendipo sindidzalira maliro.’
8Chifukwa chake miliri yake idzamugonjetsa tsiku limodzi;imfa, kulira maliro ndi njala.Iye adzanyeka ndi motopakuti wamphamvu ndi Mulungu Ambuye amene wamuweruza.
12katundu wagolide, siliva, miyala yamtengo wapamwamba ndi ngale; nsalu zoyera kwambiri zapamwamba ndi zofiira; nsalu zasilika ndi zapepo; mitengo iliyonse yonunkhira ndi zinthu zilizonse zopangidwa ndi mnyanga, kapena matabwa ogulidwa ndi ndalama zambiri kapena mkuwa kapena chitsulo ndi mwala wonyezimira;
13zokometsera zakudya, mure, lubani ndi zofukiza zina, vinyo ndi mafuta a olivi, ufa wosalala ndi tirigu; ngʼombe ndi nkhosa; akavalo ndi ngolo; ndi anthu adzagulitsidwa ukapolo.
15Amalonda amene anagulitsa zinthu izi napeza chuma kuchokera kwa iye adzayima patali potero ataopsedwa ndi mazunzo ake. Adzalira ndi kukhuza maliro
16ndipo adzalira mokuwa kuti,
16“ ‘Tsoka! Tsoka! Mzinda waukulu,iwe wovala nsalu zoyera kwambiri, zapepo ndi zofiira,ndi wonyezimira ndi golide, miyala yamtengo wapamwamba ndi ngale!
17Chuma chambiri choterechi chafika powonongeka mu ora limodzi!’
17“Oyendetsa sitima ndi onse oyenda pa sitima ya pamadzi, ogwira ntchito mʼsitima ndi onse amene amadalira nyanja pamoyo wa tsiku ndi tsiku adzayima patali potero.
22Mwa iwe simudzamvekanso liwu la woyimba zeze, ndi akatswiri a zoyimbayimba,oyimba zitoliro, ndi lipenga.Mwa iwe simudzapezekansomʼmisiri wina aliyense.Mwa iwe simudzapezekansophokoso la mphero.
23Kuwala kwa nyalesikudzawunikanso mwa inu.Mawu a mkwati ndi mkwatibwisadzamvekanso mwa iwe.Amalonda anu anali akuluakulu a dziko lapansi.Mitundu yonse inasokonezedwa ndi zamatsenga zako.
24Mwa iye munapezeka magazi a aneneri ndi a oyera mtima,ndi onse amene anaphedwa pa dziko lapansi.”