1Ndipo Mose ndi Aisraeli anayimbira Yehova nyimbo iyi: “Ine ndidzayimbira Yehovapakuti wakwezeka mʼchigonjetso.Kavalo ndi wokwera wake,Iye wawaponya mʼnyanja.
2Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;ndiye chipulumutso changa.Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamutamanda,Mulungu wa makolo anga, ine ndidzamukweza.
3Yehova ndi wankhondo;Yehova ndilo dzina lake.
4Magaleta a Farao ndi asilikali ake ankhondoIye wawaponya mʼnyanja.Akatswiri ankhondo amphamvu a Faraoamizidwa mʼNyanja Yofiira.
13Ndi chikondi chanu chosasinthika mudzatsogoleraanthu amene munawawombola.Ndi mphamvu zanu munawatsogoleraku malo anu woyera.
14Anthu amitundu ina anamva za mbiriyi ndipo ananjenjemera ndi mantha,mantha woopsa agwira anthu a dziko la Filisiti.
15Tsopano mafumu a ku Edomu agwidwa ndi mantha aakulu,otsogolera a dziko la Mowabu akunjenjemera ndi mantha,ndipo anthu a ku Kanaani asungunuka ndi mantha.
16Onse agwidwa ndi mantha woopsa.Popeza anaona mphamvu zanu zazikulu,iwo ayima chilili ngati mwala mpaka anthu anu,Inu Yehova atadutsa;inde mpaka atadutsa anthu amene munawagula.
17Inu mudzawalowetsa ndi kuwakhazikitsapa phiri lanu.Pa malo pamene Inu Yehova munawapanga kuti muzikhalapo;malo wopatulika amene Inu Ambuye munawakonza ndi manja anu.
18“Yehova adzalamulampaka muyaya.”
19Akavalo a Farao, magaleta ndi oyendetsa akavalo atalowa mʼnyanja, Yehova anawabwezera madziwo mʼnyanja ndi kuwamiza, koma Aisraeli anawoloka nyanjayo powuma.
20Ndipo Miriamu mneneri wamkazi, mlongo wa Aaroni anatenga zoyimbira ndipo akazi onse anamutsatira pambuyo, akuyimba ndi zoyimbira ndi kuvina.
21Miriamu anawayimbira nyimbo iyi:
21“Imbirani Yehova,chifukwa iye wapambana.Kavalo ndi wokwerapo wakeIye wawamiza mʼnyanja.”
22Ndipo Mose anatsogolera Israeli kuchoka ku nyanja yofiira ndi kupita ku chipululu cha Suri. Anayenda mʼchipululu masiku atatu wosapeza madzi.
23Ndipo anafika ku Mara. Koma sanathe kumwa madzi akumeneko chifukwa anali owawa. (Ndi chifukwa chake malowo amatchedwa Mara).
24Tsono anthu aja anadandaulira Mose ndi kumufunsa kuti, “Kodi tikumwa chiyani?”
25Ndipo Mose anapemphera kwa Yehova, ndipo Yehova anamuonetsa kamtengo. Iye anakaponya mʼmadzimo ndipo madzi anakhala abwino. Kumeneko Yehova anawayikira lamulo ndi maweruziro. Kumenekonso Yehova anawayesa.
26Yehova anati, “Ngati inu mudzamvetsa bwino mawu anga, kuchita zolungama, kumvera malamulo anga ndi kusamalitsa zimene ndikukuwuzani ndiye kuti Ine sindidzayika pa inu matenda amene ndinayika pa anthu a ku Igupto popeza ndine Yehova amene ndimakuchiritsani.”
27Kenaka anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe khumi ndi awiri ndi mitengo ya migwalangwa makumi asanu ndi awiri, ndipo anamanga misasa yawo kumeneko pafupi ndi madzi.