4Malire ako anali mʼkati mwenimweni mwa nyanja;amisiri ako anakukongoletsa kwambiri.
5Anakupanga ndi matabwaa payini ochokera ku Seniri;anatenga mikungudza ya ku Lebanonikupangira mlongoti wako.
6Ndi mitengo ya thundu ya ku Basanianapanga zopalasira zako;ndi matabwa a mitengo ya payini yochokera ku zilumba za Kitimu.Pakuti anapanga thandala lako pakati pa matabwawo panali minyanga ya njovu.
7Nsalu yabafuta yopeta yochokera ku Igupto inali thanga yako,ndipo inakhala ngati mbendera.Nsalu zophimba matenti ako zinali za mtundu wamtambo ndi pepozochokera ku zilumba za Elisa.
8Anthu a ku Sidoni ndi Arivadi ndi amene anali opalasa ako.Anthu aluso ako, iwe Turo, anali mwa iwe ndiwo amene ankakuyendetsa.
9Akuluakulu ndi eni luso a ku Gebala anali mʼkati mwako,ngati okonza zibowo zako.Sitima za pa nyanja zonse, ndi oyendetsa akeankabwera pamodzi ndi katundu kudzachita nawe malonda.
9
10“Anthu a ku Perisiya, a ku Ludi ndi Putianali asilikali mʼgulu lako la nkhondo.Iwo ankapachika zishango ndi zipewa zawo zankhondo pa makoma ako,kubweretsa kwa iwe ulemerero.
11Anthu a ku Arivadi ndi Helekiankalondera mbali zonse za mpanda wako;anthu a ku Gamadianali mu nsanja zako,Iwo ankapachika zishango zawo pa makoma ako onse.Amenewo ndiwo anakukongoletsa kwambiri.
12“Dziko la Tarisisi linachita nawe malonda chifukwa cha kuchuluka kwa katundu wako wamtundumtundu. Iwo ankapereka siliva, chitsulo, chitini ndi mtovu mosinthanitsa ndi katundu wako.
13“Yavani, Tubala ndi Mesaki ankachita nawe malonda; iwo ankapereka akapolo ndi ziwiya za mtovu mosinthanitsa ndi katundu wako.
14“Anthu a ku Beti Togarima ankapereka akavalo antchito, akavalo ankhondo ndi abulu mosinthanitsa ndi katundu wako.
15“Anthu a ku Dedani ankachita nawe malonda, ndipo anthu ambiri a mʼmbali mwa nyanja anali ogula malonda ako. Ankakupatsa minyanga ya njovu ndi phingo.
16“Anthu a ku Aramu ankachita nawe malonda chifukwa cha kuchuluka kwa zinthu zako. Iwo ankapereka miyala ya emeradi, nsalu zapepo, nsalu zopetapeta, nsalu zabafuta, korali ndi miyala ya rubi mosinthanitsa ndi katundu wako.
17“Yuda ndi Israeli ankachita nawe malonda. Iwo ankapereka tirigu ochokera ku Miniti ndi zokometsera zakudya, uchi, mafuta ndi mankhwala mosinthanitsa ndi katundu wako.
18“Anthu a ku Damasiko, chifukwa cha zinthu zako za malonda zambiri ndi katundu wako wosiyanasiyana, ankachita nawe malonda a vinyo wochokera ku Heliboni ndi ubweya wankhosa ochokera ku Zahari.
19Adani ndi Agriki ochokera ku Uzala ankagula katundu wako. Iwo ankapereka chitsulo chosalala, kasiya ndi bango lonunkhira mosinthanitsa ndi katundu wako.
20“Anthu a ku Dedani ankakugulitsa nsalu zoyika pa zishalo za akavalo.
21“Arabiya ndi mafumu onse a ku Kedara anali ogula malonda ako. Iwo ankachita nawe malonda a ana ankhosa onenepa, nkhosa zazimuna ndi mbuzi.
22“Anthu amalonda a ku Seba ndi Raama ankachita nawe malonda. Iwo ankapereka zonunkhira zosiyanasiyana zabwino kwambiri, miyala yokongola ndi golide mosinthanitsa ndi katundu wako.
23“Amalonda a ku Harani, Kane, Edeni, Seba, Asuri ndi Kilimadi ankachita nawe malonda.
24Iwowa ankasinthanitsana nawe zovala zokongola, nsalu zopetapeta, zoyala pansi za mawangamawanga, atazimanga bwino ndi zingwe zolimba.
25“Sitima za pa madzi za ku Tarisisi zinalizonyamula malonda ako.Motero iwe uli ngati sitima yapamadziyodzaza ndi katundu wolemera.
26Anthu opalasa ako amakupititsapa nyanja yozama.Koma mphepo yakummawa idzakuthyolathyolapakati pa nyanja.
27Chuma chako, katundu wako, malonda ako,okuyendetsa ako, okuwongolera ako ndi opanga sitima za pa madzi,anthu ako amalonda ndi asilikali ako onsendiponso aliyense amene ali mʼmenemoadzamira mʼnyanjatsiku limene udzawonongeka.
28Madera a mʼmbali mwa nyanja adzagwedezekachifukwa cha kufuwula kwa oyendetsa sitimawo.
29Onse amene amapalasa sitima zapamadzi,adzatuluka mʼsitima zawo;oyendetsa ndi onse owongolera sitima zapamadziadzayimirira mʼmbali mwa nyanja.
30Iwo akufuwula,kukulira iwe kwambiri;akudzithira fumbi kumutu,ndi kudzigubuduza pa phulusa.
31Akumeta mpala mitu yawo chifukwa cha iwendipo akuvala ziguduli.Akukulira iweyondi mitima yowawa kwambiri.
32Akuyimba nyimboyokudandaulira nʼkumati:‘Ndani anawonongedwapo ngati Turopakati pa nyanja?’
33Pamene malonda ako ankawoloka nyanjaunakhutitsa mitundu yambiri ya anthu.Mafumu a dziko lapansi analemera ndi chuma chakokomanso ndi malonda ako.
34Koma tsopano wathyokera mʼnyanja,pansi penipeni pa nyanja.Katundu wako ndi onse amene anali naweamira pamodzi nawe.
35Onse amene amakhala mʼmbali mwa nyanjaaopsedwa ndi zimene zakuchitikira.Mafumu awo akuchita manthandipo nkhope zangoti khululu.
36Anthu amalonda a mitundu ina akukunyogodola.Watha mochititsa manthandipo sudzakhalaponso mpaka muyaya.”