16Unatanganidwa ndi zamalonda.Zotsatira zake zinali zoti unachulukitsa zandewundi kumachimwa.Choncho ndinakuchotsa ku phiri langa lopatulika.Mkerubi amene ankakulondera uja anakupirikitsakukuchotsa ku miyala yamoto.
17Unkadzikuza mu mtima mwakochifukwa cha kukongola kwako,ndipo unayipitsa nzeru zakochifukwa chofuna kutchuka.Kotero Ine ndinakugwetsa pansikuti ukhala chenjezo pamaso pa mafumu.
18Ndi malonda ako achinyengo unachulukitsa machimo ako.Motero unayipitsa malo ako achipembedzo.Choncho ndinabutsa moto pakati pako,ndipo unakupsereza,ndipo unasanduka phulusa pa dziko lapansipamaso pa anthu onse amene amakuona.
19Anthu onse amitundu amene ankakudziwaakuchita mantha chifukwa cha iwe.Watheratu mochititsa manthandipo sudzakhalaponso mpaka muyaya.’ ”
20Yehova anandiyankhula nati:
21“Iwe mwana wa munthu, utembenukire ku mzinda wa Sidoni ndipo unenere mowudzudzula kuti,
22‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,
22“ ‘Ndine mdani wako, iwe Sidoni,ndipo ndidzalemekezedwa chifukwa cha iwe.Anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehovandikadzakulanga ndi kudzionetsa kutindine woyera pakati pako.
23Ndidzatumiza mliri pa iwendi kuchititsa magazi kuti ayende mʼmisewu yako.Anthu ophedwa ndi lupangaadzagwa mbali zonse.Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
24“ ‘Nthawi imeneyo Aisraeli sadzakhalanso ndi anthu pafupi achipongwe amene ali ngati nthula zowawa ndi ngati minga zopweteka. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.
25“ ‘Ine Ambuye Yehova mawu anga ndi awa: Nditasonkhanitsa Aisraeli kuchoka ku mayiko kumene anamwazikira, ndidzadzionetsa kuti ndine woyera pakati pawo pamaso pa anthu a mitundu ina. Adzakhala mʼdziko lawo, limene ndinalipereka kwa mtumiki wanga Yakobo.
26Adzakhala kumeneko mwamtendere ndipo adzamanga nyumba ndi kulima minda ya mpesa. Adzakhala kumeneko mwamtendere pamene ndidzalange anthu oyandikana nawo, amene ankawanyoza. Motero iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo.’ ”