Ezekieli 7:1-27 NYCCL2016 - Bible AI

1Yehova anandipatsa uthenga uwu kuti,

2“Iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Yehova ndikuwuza dziko la Israeli kuti:

2“Chimaliziro! Chimaliziro chafika ku ngodya zinayi za dziko.

3Chimaliziro chili pa iwe tsopano. Mkwiyo wanga ndidzawuthira pa iwe. Ndidzakuweruza molingana ndi machitidwe ako ndi kukulanga chifukwa cha zonyansa zako.

4Ine sindidzakumvera chisoni kapena kukuleka. Ndidzakulanga ndithu chifukwa cha ntchito zako zoyipa komanso chifukwa cha miyambo yako yonyansa imene ili pakati pako.

4Pamenepo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

5“Zimene ndikunena Ine Ambuye Yehova ndi izi: “Chiwonongeko! Chiwonongeko chimene sichinamvekepo! Taona chikubwera!

6Chimaliziro chafika! Chimaliziro chafika! Chiwonongeko chakugwera. Taona chafika!

7Inu anthu okhala mʼdziko, chiwonongeko chakugwerani. Nthawi yafika, tsiku layandikira; tsiku la chisokonezo osati la chimwemwe pa mapiri.

8Ine ndili pafupi kukukwiyirani, ndipo ukali wanga udzathera pa iwe; Ine ndidzakuweruza molingana ndi machitidwe ako ndiponso ndidzakulanga chifukwa cha miyambo yako yonyansa.

9Ine sindidzakumvera chisoni kapena kukuleka. Ndidzakulanga malingana ndi ntchito zako ndiponso chifukwa cha miyambo yako yonyansa pakati pako.

9‘Pamenepo udzadziwa kuti Ine Yehova ndine amene ndimakantha.’

10“Taona, tsikulo! Taona, lafika! Chiwonongeko chako chabwera. Ndodo yaphuka mphundu za maluwa. Kudzitama kwaphuka.

11Chiwawa chasanduka ndodo yowakwapulira chifukwa cha kuyipa kwawo. Palibe mwa anthu amenewo amene adzatsale. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa unyinji wawo. Palibiretu ndipo sipadzapezeka munthu wowalira maliro.

12Nthawi yafika! Tsiku layandikira! Munthu wogula asakondwere ndipo wogulitsa asamve chisoni, popeza ukali wanga uli pa gulu lonse.

13Wogulitsa sadzazipezanso zinthu zimene anagulitsa kwa wina chinkana onse awiri akanali ndi moyo, pakuti chilango chidzagwera onsewo ndipo sichingasinthike. Chifukwa cha machimo awo, palibe aliyense amene adzapulumutsa moyo wake.

13

14“Lipenga lalira, ndipo zonse zakonzeka. Koma palibe ndi mmodzi yemwe amene akupita ku nkhondo, pakuti mkwiyo wanga uli pa gulu lonse.

15Ku bwalo kuli kumenyana ndipo mʼkati muli mliri ndi njala. Anthu okhala ku midzi adzafa ndi nkhondo. Iwo okhala ku mizinda adzafa ndi mliri ndi njala.

16Onse amene adzapulumuka ndi kumakakhala ku mapiri, azidzalira ngati nkhunda za ku zigwa. Aliyense azidzabuwula chifukwa cha machimo ake.

17Dzanja lililonse lidzalefuka, ndipo bondo lililonse lidzalobodoka ngati madzi.

18Iwo adzavala ziguduli ndipo adzagwidwa ndi mantha. Adzakhala ndi nkhope zamanyazi ndipo mitu yawo adzameta mpala.

18

19“Iwo adzataya siliva wawo mʼmisewu ndipo golide wawo adzakhala chinthu chonyansa. Siliva ndi golide wawo sizidzatha kuwapulumutsa pa tsiku la ukali wa Yehova. Chuma chawochi sichidzawathandiza kuthetsa njala, kapena kukhala okhuta, pakuti ndicho chinawagwetsa mʼmachimo.

20Iwo ankanyadira zodzikongoletsera zawo zamakaka ndipo ankazigwiritsa ntchito kupanga mafano awo onyansa ndi zonyansa zawo zina. Nʼchifukwa chake Ine ndidzazisandutsa kukhala zowanyansa.

21Ndidzazipereka kwa alendo kuti azifunkhe. Anthu oyipa a dziko lapansi adzazilanda ndi kudziyipitsa.

22Ine ndidzawalekerera anthuwo ndipo adzayipitsa malo anga apamtima. Adzalowamo ngati mbala ndi kuyipitsamo.

23“Konzani maunyolo, chifukwa dziko ladzaza ndi anthu opha anzawo ndipo mzinda wadzaza ndi chiwawa.

24Ndidzabweretsa mitundu ya anthu oyipitsitsa kuti idzalande nyumba zawo. Ndidzathetsa kunyada kwa anthu amphamvu pamene anthu akunja adzalowa mʼmalo awo achipembedzo ndi kuyipitsamo.

25Nkhawa ikadzawafikira adzafunafuna mtendere koma osawupeza.

26Tsoka lidzatsatana ndi tsoka linzake, ndipo mphekesera idzatsatana ndi mphekesera inzake. Iwo adzayesa kufuna masomphenya kuchokera kwa mneneri. Adzasowa ansembe owaphunzitsa malamulo, ndipo anthu akuluakulu sadzakhalanso ndi uphungu.

27Mfumu idzalira, kalonga adzagwidwa ndi mantha. Manja a anthu a mʼdzikomo azidzangonjenjemera ndi mantha. Ine ndidzawalanga molingana ndi machitidwe awo, ndipo ndidzawaweruza molingana ndi momwe anaweruzira anzawo.

27Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

>