9Iye anali mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova; nʼchifukwa chake anthu ali ndi chisudzo, chakuti, “Ndiwe mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova monga Nimurodi.”
10Malo oyambirira a ufumu wake anali Babeli, Ereki, Akadi ndi Kaline. Malo onsewa anali mʼdziko la Sinara.
12ndi Reseni, mzinda waukulu umene uli pakati pa Ninive ndi Kala.
13Igupto ndiye kholo la Aludi, Aanami, Alehabu, Anafutu,
14Apaturusi, Akasilu ndi Akafitori (kumene kunachokera Afilisti).
14
15Kanaani anabereka mwana wake wachisamba,
15Sidoni, ndipo anaberekanso Ahiti;
16Ayebusi, Aamori, Agirigasi;
17Ahivi, Aariki, Asini,
18Aaravadi, Azemari ndi Ahamati.
18Pambuyo pake, mafuko a Akanaani anafalikira ponseponse,
19mpaka ku malire a Kanaani. Malirewo anachokera ku Sidoni kulowa cha ku Gerari mpaka ku Gaza, ndi kulowa ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa.
20Amenewa ndiwo ana aamuna a Hamu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe amakhala ndi mitundu yawo.
21Semu amene anali mkulu wake wa Yafeti nayenso anabereka nakhala kholo la Eberi.
22Ana aamuna a Semu anali: Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu.
23Ana aamuna a Aramu anali:
23Uzi, Huri, Geteri ndi Mesaki.
24Aripakisadi anabereka Sela,
24ndipo Selayo anabereka Eberi.
25A Eberi anabereka ana aamuna awiri:
25Wina anamutcha Pelegi chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani.
26Yokitani anabereka
26Alimodadi, Selefi, Hazari-Maveti, Yera,
27Hadoramu, Uzali, Dikila,
28Obali, Abimaeli, Seba,
29Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onsewa anali ana aamuna a Yokitani.
30Chigawo chimene ankakhala chinayambira ku Mesa mpaka ku Seferi, ku dera la mapiri chakummawa.
31Amenewa ndiwo ana a Semu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe ankakhala ndi mitundu yawo.
32Amenewa ndiwo mafuko a ana aamuna a Nowa monga mwa mibado ya mitundu yawo. Mitundu yonse ya anthu inatuluka mwa iwowa ndi kufalikira pa dziko lonse lapansi chitatha chigumula chija.