3Mulungu anabwera kuchokera ku Temani,Woyerayo kuchokera ku Phiri la Parani.SelaUlemerero wake unaphimba mlengalengandipo dziko lapansi linadzaza ndi matamando ake.
4Kuwala kwa ulemerero wake kunali ngati kutuluka kwa dzuwa;kunyezimira kunkatuluka mʼdzanja lake,mʼmene anabisamo mphamvu zake.
6Iye anayimirira ndi kugwedeza dziko lapansi;anayangʼana ndipo mitundu ya anthu inanjenjemera.Mapiri okhazikika anagumukandipo zitunda zakalekale zinatitimira.Njira zake ndi zachikhalire.
7Ndinaona matenti a ku Kusani ali pa mavuto,mokhala a ku Midiyani muli ululu waukulu.
7
8Inu Yehova, kodi munakwiyira mitsinje?Kodi munakalipira timitsinje?Kodi munapsera mtima nyanjapamene munakwera pa akavalo anundiponso magaleta anu achipulumutso?
9Munasolola uta wanu mʼchimake,munayitanitsa mivi yambiri.SelaMunagawa dziko lapansi ndi mitsinje;