5Anthu amene amakhala mu Samariya akuchita manthachifukwa cha fano la mwana wangʼombe ku Beti-Aveni.Anthu ake adzalirira fanolo,chimodzimodzinso ansembe ake adamawo,amene anakondwera ndi kukongola kwake,chifukwa lachotsedwa pakati pawo ndi kupita ku ukapolo.
6Fanolo lidzatengedwa kupita ku Asiriyangati mphatso kwa mfumu yayikulu.Efereimu adzachititsidwa manyazichifukwa cha mafano ake amitengo.
7Samariya ndi mfumu yake adzatengedwa kupita kutalingati kanthambi koyenda pa madzi.
8Malo opembedzerako mafano a ku Aveni adzawonongedwa.Ili ndiye tchimo la Israeli.Minga ndi mitungwi zidzamerandi kuphimba maguwa awo ansembe.Kenaka anthu adzawuza mapiri kuti, “Tiphimbeni!”ndipo adzawuza zitunda kuti, “Tigwereni!”
8
9“Iwe Israeli, wachimwa kuyambira mʼmasiku a Gibeya,ndipo wakhala uli pomwepo.Kodi nkhondo sinagonjetse anthuochita zoyipa ku Gibeya?
10Pamene ndifunire, ndidzalanga anthuwo;mitundu ya anthu idzasonkhanitsidwa kudzalimbana nawo,kuwayika mʼndende chifukwa cha uchimo wawo waukulu.
11Efereimu ndi mwana wangʼombe wamkazi wophunzitsidwaamene amakonda kupuntha tirigu,choncho Ine ndidzayika golimʼkhosi lake lokongolalo.Ndidzasenzetsa Efereimu goli,Yuda ayenera kulima,ndipo Yakobo ayenera kutipula.
12Mufese nokha chilungamondipo mudzakolola chipatso cha chikondi changa chosasinthika.Ndipo tipulani munda wanu wosalimidwawo;pakuti ino ndi nthawi yofunafuna Yehova,mpaka Iye atabwerakudzakugwetserani mivumbi ya chilungamo.
13Koma inu munadzala zolakwa,mwakolola zoyipa;mwadya chipatso cha chinyengo.Chifukwa mumadalira mphamvu zanundiponso ankhondo anu ochulukawo,
14phokoso lankhondo lidzamveka pakati pa anthu angakotero kuti malinga anu onse adzawonongeka,monga momwe Salimani anawonongera Beti-Aribeli pa nthawi ya nkhondo;pamene anapha amayi pamodzi ndi ana awo omwe.
15Momwemonso zidzakuchitikira, iwe Betelichifukwa kuyipa kwako ndi kwakukulu.Tsiku limeneli likadzafika,mfumu ya Israeli idzawonongedwa kwathunthu.