2Tsopano akunka nachimwirachimwirabe;akudzipangira mafano pogwiritsa ntchito siliva wawo,zifanizo zopangidwa mwaluso,zonsezo zopangidwa ndi amisiri.Amanena za anthu awa kuti,“Amatenga munthu ndi kumupereka nsembendipo amapsompsona fano la mwana wangʼombe.”
3Choncho adzakhala ngati nkhungu yammawa,ngati mame amene amakamuka msanga,ngati mungu wowuluka kuchokera pa malo opunthira tirigu,ngati utsi umene ukutulukira pa zenera.
3
4Koma Ine ndine Yehova Mulungu wanu,amene ndinakutulutsani mu Igupto.Simuyenera kudziwa Mulungu wina, koma Ine ndekha,palibe Mpulumutsi wina kupatula Ine.
7Motero ndidzawalumphira ngati mkango,ndidzawabisalira mu msewu ngati kambuku.
8Ngati chimbalangondo cholandidwa ana ake,ndidzawambwandira ndi kuwathyolathyola.Ndidzawapwepweta ngati mkango;chirombo chakuthengo chidzawakhadzula.
8
9“Iwe Israeli, wawonongedwa,chifukwa ukutsutsana ndi Ine, ukutsutsana ndi mthandizi wako.
10Kodi mfumu yako ili kuti, kuti ikupulumutse?Olamulira ako a mʼmizinda yonse ali kuti,amene iwe unanena za iwo kuti,‘Patseni mfumu ndi akalonga?’
11Choncho Ine ndinakupatsani mfumu mwachipseramtima,ndipo ndinayichotsa mwaukali.
12Kulakwa kwa Efereimu kwasungidwa,machimo ake alembedwa mʼbuku.
13Zowawa zonga za mayi pa nthawi yobala mwana zamugwera,koma iye ndi mwana wopanda nzeru,pamene nthawi yake yobadwa yafikaiyeyo safuna kutuluka mʼmimba mwa amayi ake.
13
14“Ndidzawapulumutsa ku mphamvu ya manda;ndidzawawombola ku imfa.Kodi iwe imfa, miliri yako ili kuti?Kodi iwe manda, kuwononga kwako kuli kuti?
14“Sindidzachitanso chifundo,
15ngakhale Efereimu akondwe pakati pa abale ake,mphepo ya kummawa yochokera kwa Yehova idzabwera,ikuwomba kuchokera ku chipululu.Kasupe wake adzaphwandipo chitsime chake chidzawuma.Chuma chake chonse chamtengowapatalichidzafunkhidwa ndipo chidzatengedwa.
16Anthu a ku Samariya adzalangidwa chifukwa cha zolakwa zawo,chifukwa anawukira Mulungu wawo.Adzaphedwa ndi lupanga;ana awo adzaphedwa mowamenyetsa pansi,akazi awo oyembekezera adzatumbulidwa pa mimba.”