Hoseya 14:1-9 NYCCL2016 - Bible AI

1Iwe Israeli bwerera kwa Yehova Mulungu wako. Machimo anu ndi amene akugwetsani!

2Bweretsani zopempha zanu ndipo bwererani kwa Yehova. Munene kwa Iye kuti, “Tikhululukireni machimo athu onse ndi kutilandira mokoma mtima, kuti tithe kukuyamikani ndi mawu a pakamwa pathu.

3Asiriya sangatipulumutse; ife sitidzakwera pa akavalo ankhondo, sitidzanenanso kuti, ‘Milungu yathu’ kwa zimene manja athu omwe anazipanga, pakuti ndinu amene mumachitira chifundo ana amasiye.”

3

4Ine ndidzachiza kusakhulupirika kwawo ndipo ndidzawakonda mwaufulu pakuti ndaleka kuwakwiyira.

5Ndidzakhala ngati mame kwa Israeli Ndipo iye adzachita maluwa ngati kakombo. Adzazika mizu yake pansi ngati mkungudza wa ku Lebanoni;

6mphukira zake zidzakula. Kukongola kwake kudzakhala ngati mtengo wa olivi, kununkhira kwake ngati mkungudza wa ku Lebanoni.

7Anthu adzakhalanso mu mthunzi wake. Iye adzakula bwino ngati tirigu. Adzachita maluwa ngati mphesa ndipo kutchuka kwake kudzakhala ngati vinyo wochokera ku Lebanoni.

8Efereimu adzati, “Ndidzachita nawonso chiyani mafano? Ine ndidzamuyankha ndi kumusamalira. Ine ndili ngati mtengo wa payini wobiriwira; zipatso zako zimachokera kwa Ine.”

8

9Ndani ali ndi nzeru? Adzazindikire zinthu izi. Ndani amene amamvetsa zinthu? Adzamvetse izi. Njira za Yehova ndi zolungama; anthu olungama amayenda mʼmenemo, koma anthu owukira amapunthwamo.

Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.
/div>