1“Nena kwa abale ako kuti, ‘Ndinu anthu anga,’ kwa alongo ako kuti ‘Ndinu okondedwa anga.’ ”
2“Dzudzulani amayi anu, adzudzuleni iwo,pakuti si mkazi wanga,ndipo ine sindine mwamuna wake.Iyeyo achotse maonekedwe adama pa nkhope yake,ndi kusakhulupirika pa mawere ake.
4Sindidzaonetsa chikondi changa pa ana ake,chifukwa ndi ana a mʼchiwerewere.
5Amayi awo akhala akuchita zachiwerewerendipo anawabereka anawo akuchita zinthu zochititsa manyazi.Iwo anati, ‘Ine ndidzatsatira zibwenzi zanga,zimene zimandipatsa chakudya ndi madzi,ubweya ndi thonje, mafuta ndi chakumwa.’
6Choncho njira yake ndidzayitseka ndi minga;ndidzamuzinga ndi khoma kotero kuti sadzapezanso njira yotulukira.
7Adzathamangira zibwenzi zake koma sadzazipeza;adzazifunafuna koma sadzazipeza.Pamenepo iye adzati,‘Ndibwerera kwa mwamuna wanga woyamba uja,pakuti ndinali pabwino ndi iyeyo kusiyanitsa ndi pano.’
8Iye sanazindikire kuti ndine amenendinkamupatsa tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta.Ndine amene ndinkamukhuthulira siliva ndi golide,zimene ankapangira mafano a Baala.
8
9“Choncho Ine ndidzamulanda tirigu wanga pa nthawi yokolola,ndi vinyo wanga watsopano pa nthawi yopsinya mphesa.Ndidzamulanda ubweya ndi thonje langa,zomwe akanaphimba nazo umaliseche wake.
10Motero tsopano ndidzaonetsa maliseche akepamaso pa zibwenzi zake;palibe ndi mmodzi yemwe adzamupulumutse mʼmanja mwanga.
11Ndidzathetsa zikondwerero zake zonse:zikondwerero zake za chaka ndi chaka, za mwezi watsopano,za pa masiku a Sabata ndi maphwando ake onse a pa masiku okhazikitsidwa.
12Ndidzawononga mitengo yake ya mpesa ndi mitengo yake yamkuyu,imene iye ankanena kuti inali malipiro ake ochokera kwa zibwenzi zake.Ndidzayisandutsa chithukuluzi,ndipo zirombo zakuthengo zidzadya zipatsozo.
13Ndidzamulanga chifukwa cha masikuamene anafukiza lubani kwa Abaala;anadzikongoletsa povala mphete ndi mikanda yamtengowapatalindipo anathamangira zibwenzi zake,koma Ine anandiyiwala,”akutero Yehova.
13
14“Koma tsopano ndidzamukopa mkaziyo;ndidzapita naye ku chipululundipo ndidzamuyankhula mwachikondi.
15Kumeneko ndidzamubwezera minda yake ya mpesa,ndipo ndidzasandutsa Chigwa cha Akori kukhala khomo la chiyembekezo.Kumeneko iye adzayimba nyimbo monga mʼmasiku a ubwana wake,monga tsiku limene anatuluka ku Igupto.