Hoseya 4:1-19 NYCCL2016 - Bible AI

1Inu Aisraeli, imvani mawu a Yehova, chifukwa Yehova ali ndi mlandu ndi inu amene mumakhala mʼdzikoli: “Mʼdziko mwanu mulibe kukhulupirika, mulibe chikondi mulibe kulabadira za Mulungu.

2Muli kutemberera kokha, kunama ndi kupha. Kuba ndi kuchita chigololo; machimo achita kunyanya ndipo akungokhalira kuphana.

3Chifukwa chake dziko likulira ndipo onse amene amakhalamo akuvutika; zirombo zakuthengo ndi mbalame zamumlengalenga ndiponso nsomba zamʼnyanja zikufa.

3

4“Koma wina asapeze mnzake chifukwa, wina aliyense asayimbe mlandu mnzake, pakuti anthu ako ali ngati anthu amene amayimba mlandu wansembe.

5Mumapunthwa usana ndi usiku ndipo aneneri amapunthwa nanu pamodzi. Choncho ndidzawononga amayi anu.

6Anthu anga akuwonongeka chifukwa chosadziwa.

6“Pakuti mwakana kudziwa, Inenso ndidzakukanani monga ansembe anga; chifukwa mwayiwala lamulo la Mulungu wanu, Inenso ndidzayiwala ana anu.

7Ansembe ankati akachuluka iwo ankandichimwiranso kwambiri; iwo anasinthanitsa ulemerero wawo ndi chinthu china chonyansa.

8Amalemererapo pa machimo a anthu anga ndipo amafunitsitsa kuti anthuwo azipitiriza kuchimwa.

9Ndipo zidzakhala motere: zochitikira anthu ena, zidzachitikiranso ansembe. Ndidzawalanga onsewo chifukwa cha njira zawo, ndidzawabwezera chifukwa cha machitidwe awo.

9

10“Iwo azidzadya koma sadzakhuta; azidzachita zachiwerewere koma sadzachulukana, chifukwa anasiya Yehova kuti adzipereke

11ku zachiwerewere, ku vinyo wakale ndi watsopano, zimene zimachotsa nzeru zomvetsa zinthu

12za anthu anga. Anthu anga amapempha nzeru ku fano lamtengo ndipo ndodo yawo yamtengo imawayankha. Mzimu wachiwerewere umawasocheretsa; iwo sakukhulupirika kwa Mulungu wawo.

13Amapereka nsembe pamwamba pa mapiri ndi kufukiza lubani pa zitunda, pa tsinde pa mtengo wa thundu, mnjale ndi mkundi, pamene pali mthunzi wabwino. Nʼchifukwa chake ana anu aakazi akuchita zachiwerewere ndipo akazi a ana anu akuchita zigololo.

13

14“Ine sindidzalanga ana anu aakazi pamene iwo adzachita zachiwerewere, kapena akazi a ana anu pamene adzachita zigololo. Paja inu nomwe amunanu mumayenda ndi akazi achiwerewere, ndipo mumapereka nsembe pamodzi ndi akazi achiwerewere a ku malo opembedzerako. Anthu amene alibe nzeru adzawonongeka ndithu!

14

15“Ngakhale umachita chigololo, iwe Israeli, Yuda asapezeke ndi mlandu wotere.

15“Usapite ku Giligala. Usapite ku Beti-Aveni. Ndipo usalumbire kuti, ‘Pali Yehova wamoyo!’

16Aisraeli ndi nkhutukumve, ngosamva ngati ana angʼombe. Kodi Yehova angathe kuwaweta bwanji ngati ana ankhosa pa msipu wabwino?

17Efereimu waphathana ndi mafano; mulekeni!

18Ngakhale pamene zakumwa zawo zatha, amapitiriza kuchita zachiwerewere; atsogoleri awo amakonda kwambiri njira zawo zochititsa manyazi.

19Adzachotsedwa ndi kamvuluvulu ndipo adzachita manyazi chifukwa cha nsembe zawo.

Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.
/div>