Hoseya 5:1-15 NYCCL2016 - Bible AI

1“Ansembe inu, imvani izi! Inu Aisraeli, tcherani khutu! Inu nyumba yaufumu, mvetserani! Chiweruzo ichi ndi chotsutsa inu: Inu munali ngati msampha ku Mizipa, munali ngati ukonde woyalidwa pa phiri la Tabori.

2Owukira azama mʼmoyo wakupha, Ine ndidzawalanga onsewo.

3Ndimadziwa zonse za Efereimu; Aisraeli ndi osabisika kwa Ine. Efereimu wayamba tsopano kuchita zachiwerewere; Israeli wadziyipitsa.

3

4“Ntchito zawo siziwalola kubwerera kwa Mulungu wawo. Mʼmitima mwawo muli mzimu wachiwerewere; Iwo sadziwa Yehova.

5Kudzikuza kwa Israeli kwakhala umboni womutsutsa; Aisraeli, ngakhale Aefereimu, anagwa mʼmachimo awo; Yudanso anagwa nawo pamodzi.

6Pamene adzapita ndi nkhosa zawo ndi ngʼombe zawo kukapereka nsembe kwa Yehova, iwo sadzamupeza; Iye wawachokera.

7Iwo ndi osakhulupirika kwa Yehova; amabereka ana amʼchigololo ndipo chikondwerero chawo cha mwezi watsopano chidzawawononga pamodzi ndi minda yawo.

7

8“Womba lipenga mu Gibeya, liza mbetete mu Rama. Fuwulani mfuwu wankhondo mu Beti-Aveni; iwe Benjamini tsogolera.

9Efereimu adzasanduka bwinja pa tsiku la chilango. Ine ndikulengeza zomwe zidzachitikadi pakati pa mafuko a Israeli.

10Atsogoleri a Yuda ali ngati anthu amene amasuntha miyala ya mʼmalire. Ndidzawakhutulira ukali wanga ngati madzi a chigumula.

11Efereimu waponderezedwa, akulangidwa chifukwa chotsatira mafano.

12Ine ndili ngati njenjete kwa Efereimu, ngati chinthu chowola kwa anthu a ku Yuda.

12

13“Efereimu ataona nthenda yake, ndi Yuda ataona zilonda zake, pamenepo Efereimu anatembenukira kwa Asiriya, ndipo anawatumizira mfumu yayikulu kudzawathandiza. Koma mfumuyo singathe kukuchizani, singathe kuchiritsa mabala anu.

14Pakuti Ine ndidzakhala ngati mkango kwa Efereimu. Ngati mkango wamphamvu kwa Yuda. Ndidzawakhadzula nʼkuchokapo; ndidzawatenga ndipo palibe amene adzawalanditse.

15Ndipo ndidzabwerera ku malo anga mpaka anthu anga atavomereza kulakwa kwawo. Ndipo iwo adzafunafuna nkhope yanga; mʼmasautso awo adzandifunitsitsa Ine.”

Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.
/div>