5Iwe Samariya, taya fano lako la mwana wangʼombe!Mkwiyo wanga wayakira anthuwo.Padzapita nthawi yayitali chotani asanasinthike kukhala oyera mtima?
6Mafanowa ndi ochokera ku Israeli!Mwana wa ngʼombe uyu anapangidwa ndi munthu waluso;si Mulungu amene anamupanga.Adzaphwanyidwa nʼkukhala zidutswa,mwana wangʼombe wa ku Samariya.
13Amapereka nsembe za nyama kwa Inendipo iwo amadya nyamayo,koma Yehova sakondwera nazo.Tsopano Iye adzakumbukira zoyipa zawondi kuwalanga chifukwa cha machimo awo:iwowo adzabwerera ku Igupto.
14Israeli wayiwala Mlengi wakendipo wamanga nyumba zaufumu;Yuda wachulukitsa mizinda ya malinga.Koma Ine ndidzaponya moto pa mizinda yawoyo,moto umene udzatenthe malinga awo.”