1Iwe Israeli, usakondwere;monga imachitira mitundu ina.Pakuti wakhala wosakhulupirika kwa Mulungu wako;umakonda malipiro a chiwerewerepa malo aliwonse opunthira tirigu.
2Malo opunthira tirigu ndi malo opsinyira mphesa sadzadyetsa anthu;adzasowa vinyo watsopano.
3Sadzakhalanso mʼdziko la Yehova.Efereimu adzabwerera ku Iguptondipo mudzadya chakudya chodetsedwa ku Asiriya.
4Iwo sadzaperekanso chopereka cha chakumwa kwa Yehova,kapena nsembe zawo kuti akondweretse Yehovayo.Nsembe zotere zidzakhala kwa iwo ngati chakudya cha anamfedwa;onse akudya chakudya chimenechi adzakhala odetsedwa.Chakudya ichi chidzakhala chodya okha,sichidzalowa mʼnyumba ya Yehova.
4
5Kodi mudzachita chiyani pa tsiku la maphwando anu oyikika;pa masiku a zikondwerero za Yehova?
6Ngakhale iwo atathawa chiwonongeko,Igupto adzawasonkhanitsa,ndipo Mefisi adzawayika mʼmanda.Khwisa adzamera pa ziwiya zawo zasiliva,ndipo minga idzamera mʼmatenti awo.
7Masiku achilango akubwera,masiku obwezera ali pafupi.Israeli adziwe zimenezi.Chifukwa machimo anu ndi ochuluka kwambirindipo udani wanu pa Mulungu ndi waukulu kwambiri.Mneneri amamuyesa chitsiru,munthu wanzeru za kwa Mulungu ngati wamisala.
8Mneneri pamodzi ndi Mulungu wangandiwo alonda a Efereimu,koma mneneri amutchera misampha mʼnjira zake zonse,ndipo udani ukumudikira mʼnyumba ya Mulungu wake.
9Iwo azama mu zachinyengomonga masiku a Gibeya.Mulungu adzakumbukira zolakwa zawondipo adzawalanga chifukwa cha machimo awo.
15“Chifukwa cha zoyipa zawo zonse ku Giligala,Ine ndinawada kumeneko.Chifukwa cha machitidwe awo auchimo,ndidzawapirikitsa mʼnyumba yanga.Sindidzawakondanso;atsogoleri awo onse ndi owukira.
16Efereimu wathedwa,mizu yake yaumasakubalanso zipatso.Ngakhale atabereka ana,Ine ndidzapha ana awo okondedwawo.”
16
17Mulungu wanga adzawakanachifukwa sanamumvere Iye;adzakhala oyendayenda pakati pa anthu a mitundu ina.