1Nthawi yomweyo, anthu miyandamiyanda atasonkhana, ndi kumapondanapondana, Yesu anayamba kuyankhula poyamba kwa ophunzira ake, nati, “Chenjereni ndi yisiti wa Afarisi, amene ndi chinyengo.
5Koma Ine ndidzakuonetsani amene muyenera kumuopa: Wopani Iye, amene pambuyo pakupha thupi, ali ndi mphamvu yakukuponyani ku gehena. Inde, Ine ndikuwuzani, muopeni Iye.
6Kodi atimba asanu samagulidwa ndi ndalama ziwiri? Ngakhale zili chomwecho palibe imodzi ya izo imene imayiwalika ndi Mulungu.
7Ndithudi, tsitsi lonse la mʼmutu mwanu ndi lowerengedwa. Musachite mantha; inu ndi oposa kwambiri mpheta zambiri.
8“Ine ndikukuwuza kuti, aliyense amene avomereza Ine pamaso pa anthu, Mwana wa Munthu adzamuvomerezanso pamaso pa angelo a Mulungu.
9Koma iye amene andikana Ine pamaso pa anthu adzakanidwanso pamaso pa angelo a Mulungu.
10Ndipo aliyense amene ayankhulira Mwana wa Munthu mawu oyipa adzakhululukidwa, koma iye wochitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa.
11“Akadzakutengerani ku masunagoge pamaso pa oweruza ndi a maulamuliro, musadere nkhawa mmene mudzadzitchinjirizire nokha kapena chimene mudzayankhule,
13Munthu wina mʼgulu la anthu anati kwa Iye, “Aphunzitsi, muwuzeni mʼbale wanga andigawireko chuma chamasiye.”
14Yesu anayankha kuti, “Munthu iwe, ndani anandiyika Ine kukhala woweruza kapena wogawa chuma pakati panu?”
15Kenaka Iye anawawuza kuti, “Chenjerani! Khalani tcheru ndi makhalidwe onse adyera; moyo wa munthu sukhala chifukwa cha kuchuluka kwa zimene ali nazo.”
16Ndipo Iye anawawuza fanizo ili, “Munda wa munthu wina wachuma unabereka kwambiri.
17Iye anaganiza kuti, ‘Ndichite chiyani? Ndilibe malo osungiramo mbewu zanga.’
18“Ndipo Iye anati, ichi ndi chimene ndidzachite: Ndidzaphwasula nkhokwe zanga zonse ndi kumanga zokulirapo, ndipo ndidzasungira mʼmenemo mbewu ndi katundu.
20“Koma Mulungu anati kwa iye, ‘Iwe wopusa! Usiku womwe uno moyo wako udzachotsedwa kwa iwe, ndipo ndi ndani amene adzatenge zimene iwe wadzikonzera?’
21“Umu ndi mmene zidzakhalire ndi aliyense amene amadziwunjikira chuma, koma si wachuma pamaso pa Mulungu.”
22Kenaka Yesu anati kwa ophunzira ake, “Choncho Ine ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu, zimene mudzadya; kapena za thupi lanu, zimene mudzavala.
36ngati anthu oyembekezera kubwera kwa mbuye wawo kuchokera kuphwando la ukwati, kuti pamene afika ndi kugogoda akhoza nthawi yomweyo kumutsekulira chitseko.
37Zidzakhala bwino kwa antchitowo amene mbuye wawo pobwera adzawapeze akudikira. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti adzakonzekera kuwatumikira, adzakhala nawo pa tebulo ndipo adzabwera ndi kuwatumikira.
38Zidzakhala bwino kwa antchitowo amene mbuye wawo adzawapeze ali okonzeka, ngakhale iye atabwera pa ora lachiwiri kapena lachitatu usiku.
39Koma zindikirani izi: Ngati mwini nyumba akanadziwa ora limene mbala ibwera, sakanalola kuti nyumba yake ithyoledwe.
40Inunso muyenera kukhala okonzeka, chifukwa Mwana wa Munthu adzabwera pa ora limene simukumuyembekezera Iye.”
41Petro anafunsa kuti, “Kodi mukunena fanizoli kwa ife, kapena kwa aliyense?”
42Ambuye anayankha kuti, “Kodi tsono woyangʼanira wokhulupirika ndi wanzeru ndani? Kodi ndi amene mbuye wake wamuyika kukhala oyangʼanira antchito ake kuti aziwapatsa ndalama yachakudya pa nthawi yake yoyenera?
43Zidzamukhalira bwino wantchito amene mbuye wake adzamupeza akuchita zimene pamene iye abwera.
44Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti adzamuyika kukhala woyangʼanira katundu wake yense.
45Koma tiyerekeze kuti wantchitoyo aziganiza mu mtima mwake kuti, ‘Bwana wanga akuchedwa kwambiri kubwera,’ ndipo kenaka ndi kuyamba kumenya antchito aamuna ndi aakazi ndi kudya, kumwa ndi kuledzera.
46Mbuye wake adzabwera tsiku limene iye sakumuyembekezera ndi ora limene iye sakudziwa. Iye adzamulanga ndi kumusiya kumalo kumene kuli osakhulupirira.
47“Wantchito amene amadziwa chifuniro cha mbuye wake koma wosakonzeka kapena wosachita chimene mbuye wake akufuna adzakwapulidwa zikwapu zambiri.