11ndipo momwemo munali mayi amene anali ndi mzimu woyipa umene unamudwalitsa zaka 18. Iye anali wokhota msana ndipo samatha kuweramuka ndi pangʼono pomwe.
12Yesu atamuona anamuyitana kutsogolo ndipo anati kwa iye, “Amayi, mwamasulidwa ku mavuto.”
13Kenaka anasanjika manja ake pa iye, ndipo nthawi yomweyo anawongoka nayamika Mulungu.
14Chifukwa cha kuyipidwa kuti Yesu anachiritsa pa Sabata, wolamulira sunagoge anati kwa anthu, “Pali masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito. Choncho bwerani kuti mudzachiritsidwe masiku amenewo osati pa Sabata.”
31Pa nthawi imeneyo Afarisi anabwera kwa Yesu ndipo anati kwa Iye, “Chokani malo ano ndipo pitani kumalo ena aliwonse. Herode akufuna kukuphani.”
32Iye anayankha kuti, “Pitani kawuzeni nkhandweyo, Ine ndikutulutsa ziwanda ndi kuchiritsa anthu lero ndi mawa ndipo tsiku lachitatu ndidzakwaniritsa cholinga changa.”
33Mʼnjira ina iliyonse, Ine ndiyenera kupitirira ulendo wanga lero, mawa ndi mkuja. Zoona nʼzakuti mneneri sangafere kunja kwa Yerusalemu.
34Iwe Yerusalemu, Yerusalemu! Umapha aneneri ndi kuwagenda miyala anthu amene atumizidwa kwa iwe. Nthawi zambiri ndakhala ndikufuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, monga nkhuku imasonkhanitsira anapiye pansi pa mapiko ake, koma iwe sunafune!
35Taona, nyumba yako yasanduka bwinja. Ine ndikukuwuza kuti, sudzandionanso mpaka pamene udzati, “Wodala amene akubwera mʼdzina la Ambuye!”