5Kenaka Iye anawafunsa kuti, “Kodi ngati mmodzi mwa inu ali ndi mwana wamwamuna kapena ngʼombe imene yagwera mʼchitsime tsiku la Sabata, kodi simungamuvuwulemo tsiku lomwelo?”
6Ndipo iwo analibe choyankha.
7Iye ataona momwe alendo amasankhira malo aulemu pa tebulo, Iye anawawuza fanizo ili:
8“Pamene wina wakuyitanani ku phwando la ukwati, musakhale pa malo aulemu ayi, chifukwa mwina anayitananso munthu wina wolemekezeka kuposa inu.
21“Wantchitoyo anabwera ndikudzamuwuza bwana wakeyo zimenezi. Pamenepo mphwandoyo anapsa mtima ndipo analamula wantchito wakeyo kuti, ‘Pita msangamsanga kunja mʼmisewu ndi mʼmakwalala a mu mzinda ndipo ukabweretse osauka, ofa ziwalo, osaona ndi olumala.’
22“Wantchitoyo anati, ‘Bwana, zimene munanena zachitika koma malo akanalipobe.’
23“Ndipo mbuye uja anawuza wantchito wake kuti, ‘Pita kunja ku misewu ikuluikulu ndi kunja kwa mpanda ndipo ukawawuze kuti alowe, kuti nyumba yanga idzaze.
24Ine ndikukuwuzani inu kuti palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu amene anayitanidwa adzalawa phwandolo.’ ”
25Gulu lalikulu la anthu linkayenda naye Yesu ndipo atatembenukira kwa iwo anati,
26“Ngati wina aliyense abwera kwa Ine ndipo sadana ndi abambo ndi amayi ake, mkazi wake ndi ana, abale ake ndi alongo ake, inde ngakhale moyo wake omwe, iye sangakhale ophunzira wanga.
27Ndipo aliyense amene sasenza mtanda wake ndi kunditsata Ine sangakhale ophunzira wanga.
28“Taganizani, ngati wina mwa inu akufuna kumanga nsanja, kodi iye sayamba wakhala pansi ndi kuganizira za mtengo wake kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kuti atsirizire?
30nanena kuti, ‘Munthu uyu anayamba kumanga koma sanathe kutsiriza.’
31“Kapena mfumu imene ikupita ku nkhondo kukamenyana ndi mfumu ina, kodi siyamba yakhala pansi ndi kulingalira ngati ingathe ndi anthu 10,000 kulimbana ndi amene akubwera ndi 20,000?
32Ngati singathe, idzatuma nthumwi pomwe winayo ali kutali ndi kukapempha mgwirizano wamtendere.
33Mʼnjira yomweyo, wina aliyense wa inu amene sasiya zonse ali nazo sangakhale ophunzira wanga.
34“Mchere ndi wabwino, koma ngati usukuluka adzawukoleretsanso ndi chiyani?
35Suyeneranso ngakhale mʼnthaka kapena kudzala la manyowa; umatayidwa kunja.