Luka 3:1-38 NYCCL2016 - Bible AI

1Mʼchaka cha 15 mu ulamuliro wa Tiberiyo Kaisara, Pontiyo Pilato ali bwanamkubwa wa Yudeya, Herode ankalamulira ku Galileya, mʼbale wake Filipo ankalamulira ku Iturea ndi ku dera la Trakoniti, ndipo Lusaniyo ankalamulira ku Abilene.

2Inalinso nthawi ya mkulu wa ansembe wa Anasi ndi Kayafa, pamene mawu a Mulungu anabwera kwa Yohane mwana wa Zakariya mʼchipululu.

3Iye anapita ku dziko lonse lozungulira mtsinje wa Yorodani, nalalikira ubatizo wa kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo.

4Monga analembera mʼbuku la Yesaya mneneri kuti:

4“Mawu a wofuwula mʼchipululu, konzani njira ya Ambuye, wongolani njira zake.

5Chigwa chilichonse chidzadzazidwa ndipo phiri lililonse ndi mtunda uliwonse zidzasalazidwa, misewu yokhotakhota idzawongoledwa, ndi njira zosasalala zidzasalazidwa.

6Ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu.”

7Yohane anati kwa magulu a anthu amene amabwera kudzabatizidwa ndi iye, “Ana anjoka inu! Anakuchenjezani ndani kuti muthawe mkwiyo umene ukubwera?

8Onetsani zipatso zakutembenuka mtima, ndipo musamanene mwa inu nokha kuti, ‘Tili nalo kholo lathu Abrahamu,’ pakuti ndikuwuzani kuti kuchokera ku miyala iyi, Mulungu akhoza kumuwutsira Abrahamuyo ana.

9Nkhwangwa ili kale pa muzu wamitengo, ndipo mtengo uliwonse umene subala chipatso chabwino udzadulidwa ndi kuponyedwa pa moto.”

10Gulu la anthuwo linafunsa kuti, “Nanga tsono tichite chiyani?”

11Yohane anayankha kuti, “Munthu amene ali ndi malaya awiri apatseko amene alibe, ndi amene ali ndi chakudya achitenso chimodzimodzi.”

12Amisonkho nawonso anabwera kudzabatizidwa. Iwo anafunsa kuti, “Aphunzitsi, ife tichite chiyani?”

13Iye anawawuza kuti, “Musalandire moposa zimene muyenera.”

14Kenaka asilikali ena anamufunsa kuti, “Nanga ife tichite chiyani?”

14Iye anayankha kuti, “Musamalande ndalama moopseza ndipo musamanamizire anthu, khutitsidwani ndi malipiro anu.”

15Anthu ankadikira ndi chiyembekezo ndipo ankasinkhasinkha mʼmitima mwawo kuti mwina Yohane nʼkukhala Khristu.

16Yohane anayankha onse kuti, “Ine ndikubatizani ndi madzi. Koma wina wondiposa ine mphamvu adzabwera amene sindili woyenera kumasula lamba wa nsapato zake. Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto.

17Mʼdzanja lake muli chopetera kuti ayeretse powomberapo tirigu ndi kusonkhanitsa tirigu ndipo adzatentha zotsalira zonse ndi moto wosazimitsika.”

18Ndipo ndi mawu ena ambiri, Yohane anawachenjeza anthu ndi kuwalalikira Uthenga Wabwino.

19Koma pamene Yohane anadzudzula Herode wolamulirayo chifukwa chokwatira Herodia, mkazi wa mʼbale wake, ndi zoyipa zina zonse anazichita,

20Herode anawonjezanso choyipa ichi pa zonsezo: Anatsekera Yohane mʼndende.

21Pamene anthu onse ankabatizidwa, Yesu anabatizidwanso. Ndipo akupemphera, kumwamba kunatsekuka.

22Mzimu Woyera anatsika pa Iye mumaonekedwe a nkhunda ndipo mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndimakondwera nawe.”

23Ndipo Yesu anali ndi zaka makumi atatu pamene anayamba ntchito yake. Monga mmene anthu ankaganizira, Iyeyo anali mwana wa Yosefe, mwana wa Heli,

24mwana wa Matate, mwana wa Yaneyi, mwana wa Yosefe

24mwana wa Levi, mwana wa Meliki,

25mwana wa Matati, mwana wa Amosi, mwana wa Nagai,

25mwana wa Naomi, mwana wa Esli,

26mwana wa Maati, mwana wa Yosefe, mwana wa Yoda

26mwana wa Matatiyo, mwana wa Simeoni,

27mwana wa Yohanani, mwana wa Resa, mwana wa Neri,

27mwana wa Zerubabeli, mwana wa Salatieli,

28mwana wa Meliki, mwana wa Elmadama, mwana wa Ere,

28mwana wa Adi, mwana wa Kosamu,

29mwana wa Jose, mwana wa Eliezara, mwana wa Levi,

29mwana wa Yorimu, mwana wa Matati,

30mwana wa Simeoni, mwana wa Yonamu, mwana wa Eliakimu,

30mwana wa Yuda, mwana wa Yosefe,

31mwana wa Meleya, mwana wa Mena, mwana wa Davide,

31mwana wa Matata, mwana wa Natani,

32mwana wa Yese, mwana wa Salimoni, mwana wa Naasoni,

32mwana wa Obedi, mwana wa Bowazi,

33mwana wa Aminadabu, mwana wa Arni, mwana wa Yuda,

33mwana wa Hezronu, mwana wa Perezi,

34mwana wa Yakobo, mwana wa Tera, mwana wa Nakoro,

34mwana wa Isake, mwana wa Abrahamu,

35mwana wa Serugi, mwana wa Reu, mwana wa Sela,

35mwana wa Pelegi, mwana wa Eberi,

36mwana wa Kainane, mwana wa Nowa, mwana wa Lameki,

36mwana wa Arfaksadi, mwana wa Semu,

37mwana wa Metusela, mwana wa Enoki, mwana wa Kainane,

37mwana wa Yaredi mwana wa Malaleeli,

38mwana wa Enosi, mwana wa Adamu, mwana wa Mulungu.

38mwana wa Seti,

Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.
iv>