1Haa! Mzinda uja wasiyidwa wokhawokha,umene kale unali wodzaza ndi anthu!Kale unali wotchuka pakati pa mitundu ya anthu!Tsopano wasanduka ngati mkazi wamasiye.Kale unali mfumukazi ya onse pa dziko lapansi,tsopano wasanduka kapolo.
2Ukulira mowawidwa mtima usiku wonse,misozi ili pa masaya pake.Mwa abwenzi ake onse,palibe ndi mmodzi yemwe womutonthoza.Abwenzi ake onse amuchitira chiwembu;onse akhala adani ake.
2
3Yuda watengedwa ku ukapolo,kukazunzika ndi kukagwira ntchito yolemetsa.Iye akukhala pakati pa anthu a mitundu ina;ndipo alibe malo opumulira.Onse omuthamangitsa iye amupitirira,ndipo alibe kwina kothawira.
3
4Misewu yopita ku Ziyoni ikulira,chifukwa palibe ndi mmodzi yemwe akubwera ku maphwando ake.Zipata zake zonse zili pululu,ansembe akubuwula.Anamwali ake akulira,ndipo ali mʼmasautso woopsa.
4
5Adani ake asanduka mabwana ake;odana naye akupeza bwino.Yehova wamubweretsera mavutochifukwa cha machimo ake ambiri.Ana ake atengedwa ukapolopamaso pa mdani.
5
6Ulemerero wonse wa mwana wamkazi wa Ziyoniwachokeratu.Akalonga ake ali ngati mbawalazosowa msipu;alibe mphamvu zothawiraowathamangitsa.
6
7Pa masiku a masautso ndi kuzunzika kwake,Yerusalemu amakumbukira chuma chonsechimene mʼmasiku amakedzana chinali chake.Anthu ake atagwidwa ndi adani ake,panalibe aliyense womuthandiza.Adani ake ankamuyangʼanandi kumuseka chifukwa cha kuwonongeka kwake.