12Mafumu a pa dziko lapansi sanakhulupirire,kapena wina aliyense wokhala pa dziko lonse,kuti adani kapena ankhondo akhoza kulowapa zipata za Yerusalemu.
12
13Koma izi zinachitika chifukwa cha kuchimwa kwa aneneri akendi mphulupulu za ansembe ake,amene ankapha anthu osalakwa pakati pawo.
13
14Tsopano akungoyendayenda mʼmisewu ya mu mzindangati anthu osaona.Iwo ndi odetsedwa kwambiri ndi magazipalibe yemwe angayerekeze nʼkukhudza komwe chovala chawo.
14
15Anthu akuwafuwulira kuti, “Chokani! Inu anthu odetsedwa!”“Chokani! Chokani! Musatikhudze ife!”Akamathawa ndi kumangoyendayenda,pakati pa anthu a mitundu yonse amati,“Asakhalenso ndi ife.”
15
16Yehova mwini wake wawabalalitsa;Iye sakuwalabadiranso.Ansembe sakulandira ulemu,akuluakulu sakuwachitira chifundo.
16
17Ndiponso maso athu atopa nʼkuyangʼana,chithandizo chosabwera nʼkomwe,kuchokera pa nsanja zathu tinadikirira mtunduwa anthu umene sukanatipulumutsa.
19Otilondola akuthamanga kwambirikuposa ziwombankhanga mu mlengalenga;anatithamangitsa mpaka ku mapirindi kutibisalira mʼchipululu.
19
20Wodzozedwa wa Yehova, mpweya wathu wotipatsa moyo,anakodwa mʼmisampha yawo.Tinaganiza kuti tidzakhala pansi pa mthunzi wakepakati pa mitundu ya anthu.
20
21Kondwera ndi kusangalala, mwana wamkazi wa Edomu.Iwe amene umakhala mʼdziko la Uzi.Koma iwenso chikho chidzakupeza;udzaledzera mpaka kukhala maliseche.
21
22Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, chilango chako chidzatha;Iye sadzatalikitsa nthawi yako ya ukapolo.Koma Yehova adzalanga machimo ako, iwe mwana wamkazi wa Edomu,ndi kuyika poyera mphulupulu zako.