1Ndipo Yesu anachoka pamalowo ndi kupita kudera la Yudeya ndi kutsidya la mtsinje wa Yorodani. Magulu a anthu anabweranso kwa Iye, ndipo monga mwachizolowezi chake anawaphunzitsa.
32Ali pa ulendo wawo wopita ku Yerusalemu, Yesu ali patsogolo, ophunzira ake anadabwa, ndipo amene amamutsatira amachita mantha. Anatenganso ophunzira ake khumi ndi awiri pa mbali ndipo anawawuza zimene zikamuchitikire Iye.
33Iye anati, “Ife tikupita ku Yerusalemu ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo. Adzamuweruza kuti aphedwe ndipo adzamupereka kwa anthu a mitundu ina,
34amene adzamuchita chipongwe ndi kumuthira malovu, kumukwapula ndi kumupha. Patatha masiku atatu adzauka.”
35Ndipo Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, anabwera kwa Iye ndipo anati, “Aphunzitsi, tikufuna kuti mutichitire ife chilichonse chimene tipemphe.”
39Iwo anayankha kuti, “Tikhoza.” Yesu anawawuza kuti, “Mudzamweradi chikho chimene Ine ndidzamwera, ndi kubatizidwa ndi ubatizo umene Ine ndidzabatizidwe nawo,
40koma kukhala kumanja kapena kumanzere si Ine wopereka. Malo awa ndi a amene anasankhidwiratu.”
41Ophunzira khumiwo otsalawo atamva izi anapsera mtima Yakobo ndi Yohane.
42Yesu anawayitana pamodzi nati, “Inu mukudziwa kuti iwo amene amadziyesa ngati atsogoleri a anthu amitundu ina amadyera anthu awo masuku pamutu. Akuluakulu awonso amaonetsadi mphamvu zawo pa iwo.
44ndipo aliyense amene akufuna kukhala wamkulu akhale kapolo wa onse.
45Pakuti ngakhale Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kuti ukhale dipo la anthu ambiri.”
46Ndipo anafika ku Yeriko. Pamene Yesu ndi ophunzira ake, pamodzi ndi gulu lalikulu la anthu, ankatuluka mu mzinda, munthu wosaona, Bartumeyu (mwana wa Tumeyu), amakhala mʼmbali mwa msewu ali kupempha.
47Pamene anamva kuti anali Yesu wa ku Nazareti, anayamba kufuwula kuti, “Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”
48Ambiri anamukalipira ndi kumuwuza kuti akhale chete, koma iye anafuwulitsabe kuti, “Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”