1Atayandikira ku Yerusalemu, anafika ku Betifage ndi Betaniya ku phiri la Olivi. Yesu anatuma awiri a ophunzira ake
2nati kwa iwo,
3
4Anapita ndipo anakapeza mwana wabulu ali kunja mu msewu waukulu atamumangirira pa chipata. Pamene anamumasula,
5anthu ena amene anayima pomwepo anafunsa kuti, “Mukuchita chiyani, kumasula mwana wabuluyo?”
6Iwo anayankha monga mmene Yesu anawawuzira, ndipo anthu aja anawalola kuti apite.
7Atafika naye mwana wabulu kwa Yesu, nayika mikanjo yawo pa buluyo, Iye anakwerapo.
8Anthu ambiri anayala mikanjo yawo pa msewu, pamene ena anayala nthambi zomwe anadula mʼminda.
9Amene anatsogola ndi iwo amene ankatsatira ankafuwula kuti,
10
11Yesu analowa mu Yerusalemu napita ku Nyumba ya Mulungu. Anayangʼana zonse, koma popeza kuti nthawi inali itapita, anatuluka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwo.
12Mmawa mwake pamene amachoka ku Betaniya, Yesu anamva njala.
13Ataonera patali mtengo wamkuyu uli ndi masamba, anapita kuti akaone ngati unali ndi chipatso chilichonse. Atafika, sanapezemo kanthu koma masamba, chifukwa sinali nthawi ya nkhuyu.
14Ndipo Iye anati kwa mtengo,
15Atafika ku Yerusalemu, Yesu analowa mʼbwalo lakunja la Nyumba ya Mulungu ndipo anayamba kupirikitsa anthu amene amagula ndi kugulitsa mʼmenemo. Anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda,
16ndipo Iye sanalole aliyense kugulitsa malonda mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu.
17Ndipo pamene ankawaphunzitsa, Iye anati,
18Akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo anamva izi ndipo anayamba kufuna njira yoti amuphere Iye, pakuti amamuopa, chifukwa gulu lonse la anthu linazizwa ndi chiphunzitso chake.
19Pofika madzulo, iwo anatuluka mu mzindamo.
20Mmamawa, pamene ankayenda, anaona mtengo wamkuyu uja utafota kuyambira ku mizu.
21Petro anakumbukira nati kwa Yesu, “Aphunzitsi, taonani! Mtengo wamkuyu munawutemberera uja wafota!”
22Yesu anayankha kuti,
23
24
25
26
27Iwo anafikanso ku Yerusalemu, ndipo pamene Yesu amayenda mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo ndi akuluakulu anabwera kwa Iye.
28Iwo anafunsa kuti, “Mukuchita izi ndi ulamuliro wanji? Ndipo anakupatsani ulamuliro umenewu ndi ndani?”
29Yesu anayankha kuti,
30
31Iwo anakambirana pakati pawo ndipo anati, “Tikati, ‘Wochokera kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga nʼchifukwa chiyani simunamukhulupirire?’
32Koma ife tikati, ‘Wochokera kwa anthu.’ ” (Amaopa anthu, pakuti aliyense amakhulupirira kuti Yohane analidi mneneri).
33Ndipo anamuyankha Yesu kuti, “Sitikudziwa.”