7Pamene mudzamva zankhondo ndi mbiri zankhondo, musadzadzidzimuke. Zinthu zotere ziyenera kuchitika, koma sikuti chimaliziro chafika kale ayi.
8Mtundu udzawukira mtundu unzake, ndi ufumu kuwukira ufumu unzake. Kudzakhala zivomerezi mʼmalo osiyanasiyana, ndi njala. Izi ndi chiyambi chabe cha zowawa monga mayi pobereka.
9“Muyenera kukhala tcheru. Mudzaperekedwa ku mabwalo oweruza ndi kukwapulidwa mwankhanza mʼmasunagoge. Mudzayima pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu monga mboni kwa iwo chifukwa cha Ine.
10Ndipo Uthenga Wabwino uyenera kuyamba walalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.
11Nthawi iliyonse pamene mwamangidwa ndi kuyimbidwa mlandu, musadandaule za zimene mudzanena. Zimene mudzapatsidwe pa nthawiyo yankhulani; pakuti sindinu amene mudzayankhula, koma Mzimu Woyera.
12“Mʼbale adzapereka mʼbale kuti aphedwe, ndipo abambo adzapereka mwana wawo. Ana adzawukira makolo awo ndi kuwapereka kuti aphedwe.
13Anthu onse adzakudani chifukwa cha Ine, koma amene adzalimbika mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.
14“Mukadzaona ‘chinthu chonyansa chosakaza’ chitayima pa malo amene si ake, owerenga azindikire. Pamenepo amene ali ku Yudeya athawire kumapiri.
15Aliyense amene ali pa denga la nyumba yake asatsike kapena kulowa mʼnyumba kukatenga kanthu kalikonse.
16Aliyense amene ali ku munda asabwerere kukatenga mkanjo wake.
17Kudzakhala koopsa mʼmasiku amenewo kwa amayi oyembekezera ndi amayi oyamwitsa!
24“Koma masiku amenewo, masautsowo atatha,“ ‘dzuwa lidzada,ndipo mwezi sudzawala;
25nyenyezi zidzagwa kuchokera ku thambo,ndipo mayiko mumlengalenga adzagwedezeka!’
26“Nthawi imeneyo anthu adzaona Mwana wa Munthu akubwera mʼmitambo ndi mphamvu yayikulu ndi ulemerero.
27Ndipo adzatuma angelo ake kukasonkhanitsa osankhidwiratu ake ku mphepo zinayi, kuyambira kumalekezero a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.
28“Tsopano phunzirani phunziro ili kuchokera ku mtengo wamkuyu. Pamene msonga za nthambi zake zikhala za nthete ndipo masamba ake ayamba kuphukira, mumadziwa kuti dzinja layandikira.
29Momwenso pamene muona zinthu izi zikuchitika, dziwani kuti wayandikira, ali pa khomo.
30Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti mʼbado uno sudzatha mpaka zinthu zonsezi zitachitika.
31Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”
32“Palibe amene akudziwa za tsikulo kapena nthawi, ngakhale angelo akumwamba, kapena Mwana, koma Atate wokha.