1Tsopano panali patatsala masiku awiri okha kuti tsiku la Paska ndi Phwando la Buledi wopanda yisiti lifike, ndipo akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ankafunafuna mpata woti amugwire Yesu ndi kumupha.
2Iwo anati, “Koma osati nthawi yaphwando, chifukwa anthu angachite chiwawa.”
3Pamene Iye anali mʼBetaniya, atakhala pa tebulo akudya mʼnyumba ya munthu wodziwika kuti Simoni wakhate, anabwera mayi ndi botolo la mafuta onunkhira amtengo wapamwamba opangidwa ndi nadi. Anaphwanya botololo nakhuthula mafutawo pa mutu wa Yesu.
4Ena mwa iwo amene analipo, anakwiya nati kwa wina ndi mnzake, “Chifukwa chiyani akuwononga mafuta onunkhirawa?
5Akanatheka kugulitsidwa ndi ndalama zambiri zoposa malipiro a pa chaka ndipo ndalamazo ndi kupatsa osauka.” Ndipo anamudzudzula iye mwaukali.
6Yesu anati,
7
8
9
10Kenaka Yudasi Isikarioti, mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anapita kwa akulu a ansembe kuti akamupereke Yesu.
11Iwo anakondwa pakumva zimenezi ndipo analonjeza kumupatsa iye ndalama. Ndipo ankadikira mpata wabwino woti amupereke.
12Pa tsiku loyamba la Phwando la Buledi wopanda yisiti, nthawi imene mwa mwambo inali ya kupha mwana wankhosa wa Paska, ophunzira a Yesu anafunsa Iye kuti, “Mufuna tipite kuti kumene tikakonzekere kuti mukadyere Paska?”
13Pamenepo anatumiza awiri mwa ophunzira ake, nawawuza kuti,
14
15
16Ophunzirawo anachoka, napita mu mzindawo ndipo anakapeza zinthu monga mmene Yesu anawawuzira. Choncho anakakonza Paska.
17Ndipo kutada Yesu anafika ndi khumi ndi awiriwo.
18Pamene ankadya pa tebulo Iye anati,
19Iwo anamva chisoni, ndipo mmodzi ndi mmodzi anati kwa Iye, “Kodi ndine?”
20Iye anayankha kuti,
21
22Pamene ankadya, Yesu anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema nagawira ophunzira ake nanena kuti,
23Kenaka anatenga chikho, nayamika nachipereka kwa iwo ndipo onse anamweramo.
24Iye anawawuza kuti,
25
26Atayimba nyimbo, anapita ku phiri la Olivi.
27Yesu anati,
28
29Petro anati, “Ngakhale onse adzakuthaweni, ine sindidzatero.”
30Yesu anayankha kuti,
31Koma Petro ananenetsa kuti, “Ngakhale kutakhala kufa nanu, ine sindidzakukanani.” Ndipo ena onse ananena chimodzimodzi.
32Ndipo anapita ku malo otchedwa Getsemani, ndipo Yesu anati kwa ophunzira ake,
33Iye anatenga Petro, Yakobo ndi Yohane, ndipo anayamba kumva chisoni kwambiri ndi kuvutika mu mtima.
34Iye anawawuza kuti,
35Atapita patsogolo pangʼono, anagwa pansi ndi kupemphera kuti ngati ndi kotheka oralo limupitirire.
36Iye anati,
37Kenaka anabwerera kwa ophunzira ake ndipo anawapeza akugona, Iye anati kwa Petro,
38
39Kenakanso anachoka ndi kukapemphera chimodzimodzi.
40Iye atabwerera, anawapezanso akugona, chifukwa mʼmaso mwawo munadzaza tulo. Iwo sanadziwe choti anene kwa Iye.
41Atabweranso kachitatu, anawafunsa kuti,
42
43Iye akuyankhulabe, Yudasi, mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anatulukira. Anali ndi gulu la anthu litanyamula malupanga ndi zibonga, otumidwa ndi akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo, ndi akuluakulu.
44Tsopano womupereka anapangana chizindikiro ndi iwo kuti: “Amene ndikapsompsone ndi iyeyo; mukamugwire ndi kumutenga ali womangidwa.”
45Atapita kwa Yesu nthawi yomweyo, Yudasi anati, “Aphunzitsi,” ndipo anapsompsona.
46Anthu anamugwira Yesu ndi kumumanga.
47Kenaka mmodzi wa iwo amene anayima pafupipo anatulutsa lupanga lake nakhapa wantchito wa wamkulu wa ansembe, nʼkudula khutu lake.
48Yesu anati,
49
50Pamenepo ophunzira ake onse anathawa namusiya yekha.
51Mnyamata wamngʼono amene anangofundira nsalu yokha, wopanda chovala ankamutsatira Yesu. Atamugwira,
52anathawa wamaliseche kusiya nsalu yake mʼmbuyo.
53Anamutengera Yesu kwa mkulu wa ansembe, ndipo akulu a ansembe, akuluakulu ndi aphunzitsi amalamulo anasonkhana pamodzi.
54Petro anamutsatira ali patali, mpaka ku bwalo la mkulu wa ansembe. Kumeneko anakhala pansi ndi alonda namawotha moto.
55Akulu a ansembe ndi onse olamulira a Ayuda ankafunafuna umboni womutsutsa Yesu kuti amuphe, koma sanapeze wina uliwonse.
56Ambiri anamunenera Iye maumboni abodza, koma maumboni awo sanagwirizane.
57Kenaka ena anayimirira namunenera umboni wonama womutsutsa Iye kunena kuti,
58“Tamumva akunena kuti, ‘Ndidzawononga Nyumba ya Mulungu iyi yopangidwa ndi anthu ndipo mʼmasiku atatu ndidzamanga ina, osati yopangidwa ndi munthu.’ ”
59Ngakhale iwonso umboni wawo sunagwirizane.
60Kenaka mkulu wa ansembe anayimirira pakati pawo namufunsa Yesu kuti, “Kodi suyankha? Kodi umboni uwu ndi wotani umene anthu akukuchitira?”
61Koma Yesu anakhala chete ndipo sanayankhe.
62Yesu anati, “Ndine, ndipo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala kudzanja lamanja la Wamphamvuzonse ndipo akubwera mʼmitambo ya kumwamba.”
63Mkulu wa ansembe anangʼamba zovala zaunsembe zake. Iye anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani tikufuna mboni zinanso?
64Mwamva mwanowo. Muganiza chiyani?”
65Kenaka ena anayamba kumulavulira malovu; anamumanga mʼmaso, namumenya ndi zibakera ndipo anati, “Nenera!” Ndipo asilikali anamutenga namumenya.
66Petro ali chakumunsi kwa bwalo la milandu, mmodzi wa atsikana a ntchito a mkulu wa ansembe anabwera.
67Ataona Petro akuwotha moto, anamuyangʼanitsitsa.
68Koma iye anakana nati, “Sindikudziwa kapena kumvetsetsa zimene ukuyankhula.” Ndipo anachoka napita ku chipata.
69Pamene mtsikana wantchitoyo anamuona iye, anatinso kwa iwo amene anayimirira pomwepo, “Munthu uyu ndi mmodzi mwa iwo.”
70Anakananso kachiwiri.
71Iye anayamba kudzitemberera, nalumbira kuti, “Sindimudziwa munthu ameneyu.”
72Nthawi yomweyo tambala analira kachiwiri. Pamenepo Petro anakumbukira mawu amene Yesu ananena anamuwuza kuti,