1Ndipo anawawuza kuti,
2Patatha masiku asanu ndi limodzi Yesu anatenga Petro, Yakobo ndi Yohane nawatsogolera kupita ku phiri lalitali, kumene anali okhaokha. Kumeneko maonekedwe ake anasinthika pamaso pawo.
3Zovala zake zinawala monyezimira kwambiri, kotero kuti palibe sopo wina aliyense amene angaziyeretse monyezimira chotere pa dziko la pansi.
4Ndipo anaonekera Eliya ndi Mose pamaso pawo, amene ankayankhulana ndi Yesu.
5Petro anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, ndi kwabwino kuti ife tili pano. Tiyeni timange misasa itatu; umodzi wanu, wina wa Mose ndi wina wa Eliya.”
6(Iye sanadziwe choti anene, anali ndi mantha akulu).
7Pamenepo mtambo unaoneka ndi kuwaphimba, ndipo mawu anamveka kuchokera mu mtambo kuti, “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa. Mvereni Iye!”
8Mwadzidzidzi, atayangʼanayangʼana, sanaonenso wina aliyense ali ndi iwo kupatula Yesu.
9Pamene ankatsika kuchokera ku phiri, Yesu anawalamulira kuti asawuze aliyense zimene anaona mpaka Mwana wa Munthu atauka kwa akufa.
10Iwo anayisunga nkhaniyo nakambirana za tanthauzo lake la “Kuuka kwa akufa.”
11Ndipo anamufunsa Iye kuti, “Nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amati Eliya ayenera kuyamba wabwera?”
12Yesu anayankha kuti,
13
14Atafika kwa ophunzira ena aja, anaona gulu lalikulu la anthu litawazungulira ndi aphunzitsi amalamulo akutsutsana nawo.
15Nthawi yomweyo anthu onse atamuona, anadabwa kwambiri ndipo anathamanga kukamulonjera.
16Iye anafunsa kuti,
17Munthu wina mʼgululo anayankha kuti, “Aphunzitsi, ndinakubweretserani mwana wanga wamwamuna, amene ndi ogwidwa ndi mzimu umene umamulepheretsa kuyankhula.
18Nthawi iliyonse ukamugwira umamugwetsa pansi. Amatuluka thovu kukamwa, amakukuta mano ake ndipo amawuma. Ndinapempha ophunzira anu kuti awutulutse mzimuwo, koma sanathe.”
19Yesu anayankha kuti,
20Ndipo anamubweretsa kwa Iye. Mzimu woyipawo utaona Yesu, nthawi yomweyo unamukomola mnyamatayo. Anagwa pansi ndi kumagubuduka, ndi kuchita thovu kukamwa.
21Yesu anafunsa abambo a mnyamatayo kuti,
22wakhala ukumuponya pa moto kapena mʼmadzi kuti umuphe. Koma ngati mungathe kuchita kanthu, tichitireni chifundo ndipo mutithandize.”
23Yesu anati,
24Nthawi yomweyo abambo a mwanayo anafuwula kuti, “Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga!”
25Yesu ataona kuti gulu la anthu likuthamangira kumalowo, anadzudzula mzimu woyipawo kuti,
26Mzimuwo unafuwula ndi kumugubuduza kwambiri ndipo unatuluka. Mnyamatayo anaoneka ngati mtembo ndipo ambiri anati, “Wafa.”
27Koma Yesu anamugwira dzanja ndipo anamuyimiritsa, ndipo anayimirira.
28Yesu atalowa mʼnyumba, ophunzira ake anamufunsa ali pa okha kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani ife sitinathe kutulutsa chiwandacho?”
29Iye anayankha kuti,
30Anachoka malo amenewo nadutsa ku Galileya. Yesu sanafune kuti wina aliyense adziwe kumene anali,
31chifukwa amaphunzitsa ophunzira ake. Anati kwa iwo,
32Koma sanazindikire chimene amatanthauza, ndipo anachita mantha kuti amufunse.
33Anafika ku Kaperenawo. Pamene anali mʼnyumba, anawafunsa kuti,
34Koma anakhala chete chifukwa ali mʼnjira amatsutsana za kuti wamkulu kuposa onse ndani.
35Atakhala pansi, Yesu anayitana khumi ndi awiriwo nati,
36Anatenga kamwana nakayimiritsa pakati pawo ndipo anawawuza kuti,
37
38Yohane anati, “Aphunzitsi, tinaona munthu akutulutsa ziwanda mʼdzina lanu ndipo ife tinamuwuza kuti aleke, chifukwa sanali mmodzi wa ife.”
39Yesu anati,
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50