Masalimo 101:1-8 NYCCL2016 - Bible AI

1Salimo la Davide. Ndidzayimba za chikondi ndi chiweruzo chanu cholungama; kwa Inu Yehova ndidzayimba matamando.

2Ndidzatsata njira yolungama; nanga mudzabwera liti kwa ine?

2Ndidzayenda mʼnyumba mwanga ndi mtima wosalakwa.

3Sindidzayika chinthu chilichonse choyipa pamaso panga.

3Ine ndimadana ndi zochita za anthu opanda chikhulupiriro; iwo sadzadziphatika kwa ine.

4Anthu a mtima wokhota adzakhala kutali ndi ine; ine sindidzalola choyipa chilichonse kulowa mwa ine.

4

5Aliyense wosinjirira mnansi wake mseri ameneyo ndidzamuletsa; aliyense amene ali ndi maso amwano ndi mtima wodzikuza, ameneyo sindidzamulekerera.

5

6Maso anga adzakhala pa okhulupirika mʼdziko, kuti akhale pamodzi ndi ine; iye amene mayendedwe ake ndi wosalakwa adzanditumikira.

6

7Aliyense wochita chinyengo sadzakhala mʼnyumba mwanga. Aliyense woyankhula mwachinyengo sadzayima pamaso panga.

7

8Mmawa uliwonse ndidzatontholetsa anthu onse oyipa mʼdziko; ndidzachotsa aliyense wochita zoyipa mu mzinda wa Yehova.

e>