1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.Mwa Yehova ine ndimathawiramo.Nanga mungathe bwanji kunena kwa ine kuti,“Thawira ku phiri lako ngati mbalame.
2Pakuti taona oyipa akunga mauta awo;ayika bwino mivi yawo pa zingwe za uta,pobisala pawo kuti alaseolungama mtima.