Masalimo 111:1-10 NYCCL2016 - Bible AI

1Tamandani Yehova. Ndidzathokoza Yehova ndi mtima wanga wonse mʼbwalo la anthu olungama mtima ndi pa msonkhano.

2Ntchito za Yehova nʼzazikulu; onse amene amakondwera nazo amazilingalira.

3Zochita zake ndi za ulemerero ndi zaufumu, ndipo chilungamo chake ndi chosatha.

4Iye wachititsa kuti zodabwitsa zake zikumbukirike; Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo.

5Amapereka chakudya kwa amene amamuopa Iye; amakumbukira pangano lake kwamuyaya.

6Waonetsa anthu ake mphamvu ya ntchito zake, kuwapatsa mayiko a anthu a mitundu ina.

7Ntchito za manja ake ndi zokhulupirika ndi zolungama; malangizo ake onse ndi odalirika.

8Malamulo ndi okhazikika ku nthawi za nthawi, ochitidwa mokhulupirika ndi molungama.

9Iyeyo amawombola anthu ake; anakhazikitsa pangano lake kwamuyaya dzina lake ndi loyera ndi loopsa.

9

10Kuopa Yehova ndicho chiyambi cha nzeru; onse amene amatsatira malangizo ake amamvetsa bwino zinthu. Iye ndi wotamandika mpaka muyaya.

le>