Masalimo 112:1-10 NYCCL2016 - Bible AI

1Tamandani Yehova. Wodala munthu amene amaopa Yehova, amene amakondwera kwambiri ndi malamulo ake.

2Ana ake adzakhala amphamvu mʼdziko; mʼbado wa olungama mtima udzadalitsidwa.

3Kulemera ndi chuma zili mʼnyumba yake, ndipo chilungamo chake ndi chosatha.

4Ngakhale mu mdima kuwala kumatulukira olungama mtima; wokoma mtima, wachifundo ndi wowongoka mtima.

5Zinthu zabwino zidzabwera kwa iye amene amapereka mowolowamanja ndi wokongoletsa mwaufulu, amene amachita ntchito yake mwachilungamo.

5

6Ndithu sadzagwedezeka; munthu wolungama sadzayiwalika mpaka muyaya.

7Saopa akamva zoyipa zimene zachitika; mtima wake ndi wokhazikika ndipo amadalira Yehova.

8Mtima wake ndi wotetezedwa, sadzakhala ndi mantha; potsiriza pake adzayangʼana adani ake mwachipambano.

9Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka, chilungamo chake chimanka mpaka muyaya; nyanga yake idzakwezedwa mwaulemu.

9

10Munthu woyipa adzaona zimenezi ndipo adzapsa mtima; adzakukuta mano ake ndipo adzasungunuka. Zolakalaka za anthu oyipa sizidzachitika konse.

le>