1Tamandani Yehova. Mutamandeni, inu atumiki a Yehova, tamandani dzina la Yehova.
2Yehova atamandidwe, kuyambira tsopano mpaka muyaya.
3Kuyambira ku matulukiro a dzuwa mpaka ku malowero ake, dzina la Yehova liyenera kutamandidwa.
3
4Yehova wakwezeka pa anthu a mitundu yonse, ulemerero wake ndi woposa mayiko akumwamba.
5Ndani wofanana ndi Yehova Mulungu wathu, Iye amene amakhala mwaufumu mmwamba?
6amene amawerama pansi kuyangʼana miyamba ndi dziko lapansi?
6
7Iye amakweza munthu wosauka kuchoka pa fumbi ndi kutukula munthu wosowa kuchoka pa dzala;
8amawakhazika pamodzi ndi mafumu, pamodzi ndi mafumu a anthu ake.
9Amakhazikitsa mayi wosabereka mʼnyumba yake monga mayi wa ana wosangalala.