1Pamene Israeli anatuluka mu Igupto, nyumba ya Yakobo kuchoka ku mtundu wa anthu a chiyankhulo chachilendo,
2Yuda anasanduka malo opatulika a Mulungu, Israeli anasanduka ufumu wake.
2
3Nyanja inaona ndi kuthawa, mtsinje wa Yorodani unabwerera mʼmbuyo;
4mapiri analumphalumpha ngati nkhosa zazimuna, timapiri ngati ana ankhosa.
4
5Nʼchifukwa chiyani iwe unathawa? iwe mtsinje wa Yorodani unabwereranji mʼmbuyo?
6inu mapiri, munalumphalumphiranji ngati nkhosa zazimuna, inu timapiri, ngati ana ankhosa?
6
7Njenjemera pamaso pa Ambuye iwe dziko lapansi, pamaso pa Mulungu wa Yakobo,
8amene anasandutsa thanthwe kukhala chitsime, thanthwe lolimba kukhala akasupe a madzi.