Masalimo 120:1-7 NYCCL2016 - Bible AI

1Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndimafuwulira kwa Yehova mʼmasautso anga, ndipo Iye amandiyankha.

2Pulumutseni Yehova ku milomo yabodza, ndi kwa anthu achinyengo.

2

3Kodi adzakuchitani chiyani, ndipo adzawonjezerapo zotani, inu anthu achinyengo?

4Adzakulangani ndi mivi yakuthwa ya munthu wankhondo, ndi makala oyaka a mtengo wa tsanya.

4

5Tsoka ine kuti ndimakhala ku Mesaki, kuti ndimakhala pakati pa matenti a ku Kedara!

6Kwa nthawi yayitali ndakhala pakati pa iwo amene amadana ndi mtendere.

7Ine ndine munthu wamtendere; koma ndikamayankhula, iwo amafuna nkhondo.

e>