1Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndikweza maso anga ku mapiri; kodi thandizo langa limachokera kuti?
2Thandizo langa limachokera kwa Yehova, wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
2
3Sadzalola kuti phazi lako literereke; Iye amene amakusunga sadzawodzera.
4Taonani, Iye amene amasunga Israeli sadzawodzera kapena kugona.
4
5Yehova ndiye amene amakusunga; Yehova ndiye mthunzi wako ku dzanja lako lamanja.
6Dzuwa silidzakupweteka nthawi ya masana, kapena mwezi nthawi ya usiku.
6
7Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse; adzasunga moyo wako.
8Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako; kuyambira tsopano mpaka muyaya.