Masalimo 122:1-9 NYCCL2016 - Bible AI

1Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndinakondwera atandiwuza kuti, “Tiyeni ku nyumba ya Yehova.”

2Mapazi athu akuyima mʼzipata zako, Iwe Yerusalemu.

2

3Yerusalemu anamangidwa ngati mzinda umene uli wothithikana pamodzi.

4Kumeneko ndiye kumene kumapita mafuko, mafuko a Yehova, umboni wa kwa Israeli, kuti atamande dzina la Yehova.

5Kumeneko anayikako mipando yaufumu yachiweruzo, mipando yaufumu ya nyumba ya Davide.

5

6Pemphererani mtendere wa Yerusalemu: “Iwo amene amakukonda iwe zinthu ziwayendere bwino.

7Mukhale mtendere mʼkati mwa makoma ako, ndipo mʼnyumba zako zaufumu mukhale chitetezo.”

8Chifukwa cha abale anga ndi abwenzi anga ndidzati, “Mtendere ukhale mʼkati mwako.”

9Chifukwa cha Nyumba ya Yehova Mulungu wathu, ndidzakufunira zabwino.

e>