1Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndikweza maso anga kwa Inu, kwa Inu amene mumakhala kumwamba.
2Taonani, monga momwe maso a akapolo amayangʼana mʼdzanja la mbuye wawo, monga momwenso maso a mdzakazi amayangʼana mʼdzanja la dona wake, choncho maso athu ali kwa Yehova Mulungu wathu, mpaka atichitire chifundo.