1Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova, anene tsono Israeli,
2akanapanda kukhala mbali yathu Yehova, potiwukira anthuwo,
3iwo atatipsera mtima, akanatimeza amoyo;
4chigumula chikanatimiza, mtsinje ukanatikokolola,
5madzi a mkokomo akanatikokolola.
5
6Atamandike Yehova, amene sanalole kuti tikhale chakudya cha mano awo.
7Moyo wathu wawonjoka ngati mbalame yokodwa mu msampha wa mlenje; msampha wathyoka, ndipo ife tapulumuka.
8Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.