1Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Amene amadalira Yehova ali ngati phiri la Ziyoni, limene silingagwedezeke koma ndi lokhala mpaka muyaya.
2Monga mapiri azungulira Yerusalemu, momwemonso Yehova azungulira anthu ake kuyambira tsopano mpaka muyaya.
2
3Ndodo yaufumu ya anthu oyipa sidzakhala pa dziko limene lapatsidwa kwa anthu olungama, kuti anthu olungamawo angachite nawonso zoyipa.
3
4Yehova chitirani zabwino amene ndi abwino, amene ndi olungama mtima
5Koma amene amatembenukira ku njira zokhotakhota, Yehova adzawachotsa pamodzi ndi anthu ochita zoyipa.
5Mtendere ukhale pa Israeli.