1Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Odala ndi onse amene amaopa Yehova, amene amayenda mʼnjira zake.
2Udzadya chipatso cha ntchito yako; madalitso ndi chuma zidzakhala zako.
3Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka mʼkati mwa nyumba yako; ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi kuzungulira tebulo lako.
4Ameneyu ndiye munthu wodalitsidwa amene amaopa Yehova.