Masalimo 129:1-8 NYCCL2016 - Bible AI

1Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. “Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,” anene tsono Israeli;

2“Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga, koma sanandipambane.

3Anthu otipula analima pa msana panga ndipo anapangapo mizere yayitali:

4Koma Yehova ndi wolungama; Iye wandimasula ku zingwe za anthu oyipa.”

4

5Onse amene amadana ndi Ziyoni abwezedwe pambuyo mwamanyazi.

6Akhale ngati udzu womera pa denga la nyumba, umene umafota usanakule;

7sungadzaze manja a owumweta kapena manja a omanga mitolo.

8Odutsa pafupi asanene kuti, “Dalitso la Yehova lili pa inu; tikukudalitsani mʼdzina la Yehova.”

e>