1Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndikulirira kwa Inu Yehova ndili mʼdzenje lozama;
2Ambuye imvani mawu anga. Makutu anu akhale tcheru kumva kupempha chifundo kwanga.
2
3Inu Yehova, mukanamawerengera machimo, Inu Yehova, akanayima chilili ndani wopanda mlandu?
4Koma kwa Inu kuli chikhululukiro; nʼchifukwa chake mumaopedwa.
4
5Ndimayembekezera Yehova, moyo wanga umayembekezera, ndipo ndimakhulupirira mawu ake.
6Moyo wanga umayembekezera Ambuye, kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa, inde, kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,
6
7Yembekeza Yehova, iwe Israeli, pakuti Yehova ali ndi chikondi chosasinthika ndipo alinso ndi chipulumutso chochuluka.
8Iye mwini adzawombola Israeli ku machimo ake onse.