5Ndikudziwa kuti Yehova ndi wamkulu,kuti Ambuye athu ndi wamkulu kuposa milungu yonse.
6Yehova amachita chilichonse chimene chimamukomera,kumwamba ndi dziko lapansi,ku nyanja zazikulu ndi ku malo ake onse akuya.
7Iye amatulutsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi,amatumiza zingʼaningʼani pamodzi ndi mvulandipo amatulutsa mphepo ku malo ake osungiramo.
7
8Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto,ana oyamba kubadwa a anthu ndi nyama.
9Iye anatumiza zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa pakati pako, iwe Igupto,kutsutsana ndi Farao pamodzi ndi atumiki ake onse.
10Iye anakantha mitundu yambiri ya anthundi kupha mafumu amphamvu:
11Sihoni mfumu ya Aamori,Ogi mfumu ya Basani,ndi maufumu onse a ku Kanaani;
12ndipo anapereka dziko lawo ngati cholowa,cholowa cha anthu ake Aisraeli.
12
13Dzina lanu, Inu Yehova, ndi losatha mpaka muyaya,mbiri yanu, Inu Yehova, idziwika mibado yonse.